Mutu 26

1 Chinabwela chachitika kuti pamene Yesu anasiliza mau yonse, Ananena ku bophunzila bake, 2 "Muziba kuti kuchokela masiku awiri Pasaka ilikubwela, ndiponso mwana wa munthu azapelekewa mu kupachikiwa.'' 3 Ndipo mukulu wabakulu bansembe nabakulu ba banthu banabwela pamodzi mumalo yaopeleka bansembe, wamene analikuitanidwa zina Kayafasi. 4 Banapangana kuti bamugwire mobisa ndiponso nakumupaya. 5 Chifukwa banalikunena kuti, ''Osati nthawi yaphwando chifukwa pangauke chongo pakati pa banthu.'' 6 Manje Yesu anali ku Betaniya munyumba ya Simoni wa khate, 7 pamene anali anasamila pa tebulo, muzimayi wina anabwera kuli eve na botolo ya mafuta yonunkhira ya mtengo wapatali, ndiponso anayatila pamuthu wake. 8 Koma pamene bophunzila bake banaona ichi, banabwela bakalipa ndikunena kuti, ''Nichifukwa chani ulikuonongela? 9 Sembe mafuta yamene aya yagulisiwa pa mutengo ukulu, ndipo izi ndalama sembe zapasiwa kuosauka.'' 10 Koma Yesu, poziba izi, anakamba kuli beve, ''Nichifukwa chani muvutisila muzimayi uyu? 11 Chifukwa achita chinthu chabwino kuli ine. Mumankhala nabosauka nthawi zonse, Koma simuzankhala naine nthawi zonse. 12 13 Koma pamene anathira mafuta yonunkhila pa thupi langa, achita izi kukonzeka kufwikiliwa kwanga. Nikuuzani zoona, kulikonse kwamene utenga uzalalikiwa muno muziko, chamene uyu muzimayi achita chizakakambiwapo mukukumbukila uyu muzimayi.'' 14 Ndipo umodzi wa kumi na yabiri palibeve oitaniwa Yudasi Isikarioti, anapita kuli akulu ansembe nakufunsa kuti, 15 ''Kodi nichani chamene muzanipasa ngati namubwelesa kuli imwe?'' Banapima ndalama zokwanila masiliva makumi yatatu. 16 Kuyambira pamene paja banasakila nthawi yabwino yopeleka Yesu kulibeve. 17 Pa siku yoyamba yaphwando ya mukate yamene ilibe chotupisa bophunzila banabwela kuli Yesu nakunena ati? '' Kodi nikuti kwamene mufuna kuti tikakukonzekele malo yodyelamo pasakha?'' 18 Anabauza kuti, "Yendani mumuzinda ku mwamuna wina ndiponso mumuuze kuti, 'Mupunzisi anena kuti, ''Nthawi yanga yafika. Nizasunga pasakha pa nyumba yako pamozi na bophunzila banga.'' 19 Bophunzila banachita mwamene Yesu anabauzila, ndiponso banakonza chakudya cha Pasakha. 20 Pamene chinafika kumazulo, Yesu anankhala pansi na bophunzila bake khumi na yabiri na kudya. 21 Pamene banali kudya, anakamba, ''Nikuuzani zoona imwe kuti umodzi pali imwe azanigulisa.'' 22 Banamvesewa chisoni, ndiponso wina wache anayamba kumufunsa eve, ''Nditu ine sindine, Ambuye?'' 23 Anayankha ati, ''Wamene aza ngenesa kwanja kwake pamodzi na ine mubeseni ndiye wamene azanigulisa. 24 Mwana wa Munthu azayenda, monga mwamene chinalembedwa pali eve. Koma soka kuli uja munthu wamene azamugulisa! Chinawama ngati uja munthu sanabadwe.'' 25 Yuda, wamene enzo yenera kumugulisa anati, '' Kodi ndine, Muphunzisi?'' Anamuuza ati, '' Wazikambila iwe weka.'' 26 Pamene benze bakalikudya, Yesu anatenga mukhate, nakuudalisa, ndiponso anaigomola. Anapasako bophunzila bake nakukamba ati, ''Tengani, mudye. Iyi ndiye thupi yanga.'' 27 Anatenga kapu nakuyamika, Ndiponso anabapasa na kukamba ati, "Mwani, imwe bonse. 28 Chifukwa uyu ndiye mwazi wanga wachipangano wamene unatikiwa kukhululukila machimo ya bambiri. 29 Koma nikuuzani, Sinizakamwapo futi ku chipatso cha mutengo wampesa, mpaka siku yamene nizakamwa mwasopano na imwe mu ufumu wa Batate banga.'' 30 Pamene banaimba nyimbo, banayenda kuphiri ya Olive. 31 Koma Yesu anati kuli beve, "Imwe bonse muzagwa usiku uno chifukwa chaine, chifukwa chinalembedwa, 'Nizakwapula mubusa ndiponso nkhosa zizamwazikana.' 32 Koma pamene nizauka, nizayenda pasogolo painu mu Galileya.'' 33 Koma Petulo anakamba kuti, ''Chingankhale kuti bonse bagwa chifukwa chaimwe, ine sinizagwapo.'' 34 Yesu anati kuli eve, ''Nikuuza zoona kuti, lelo usiku pamene kombwe akalibe nakulila, uzanikana katatu.'' 35 Petulo anakamba kuli eve ati, ''Chingankhakele kuti ningafele pamozi naimwe, Sinizakukanani.'' Bonse bophunzila bake banakamba chimodzimodzi. 36 Koma Yesu anayenda na beve kumalo yoitaniwa Getesemani ndiponso anakamba kubophunzila bake, ''Nkhalani pamenepano, pamene paja apo, pamene niyenda mukupempela.'' 37 Anatenga Petulo na bana babili ba Zebedi na eve ndiponso anayamba kunkhala na chisoni na kuvutikiwa mutima. 38 Ndipo anakamba kuli beve ati, ''Moyo wanga wazuliwa na chisoni, chakufa nacho. Nkhalani pamenepano ndiponso yanganilani na ine.'' 39 Anayendanso pang'ono pasogolo, anagwesa nkhope na kupempela. Anakamba ati, ''Tate wanga, ngati nichoteka, lekani iyi kapu inipitilile. Koma, osati kulinganiza nakufuna kwanga, Koma kulinganiza nachifunilo chanu.'' 40 Anabwela kubophunzila bake ndiponso anapeza baligone, ndiponso anauza Petulo, ''Nichifukwa chani simunga yanganile na ine ora imodzi? 41 Yanganilani na kupempela kuti musagwele mu mayeso. Muzimu ufuna, koma thupi ni yofokela.'' 42 Anayendanso kachibiri mukupempela. Anakamba kuti, ''Tate wanga, ngati ichi sichinganipilile koma chabe nimwe, chifuniro chanu chichitike.'' 43 Anabwelanso nakupeza bakaligone, chifukwa manso yabo yanali yolema. 44 Pamene anabasiyanso, anayenda kupempela ka chitatu, ndikunena mau yamodzimodzi. 45 Ndipo Yesu anabwela kubophunzila bake na kubauza ati, ''Mukaligone na kupumula? Onani, ora ili pafupi, ndiponso Mwana wa Munthu azagulisiwa mu manja yabochimwa. 46 Nyamukani, tiyeni tiyende. Onani, onigulisa alipafupi.'' 47 Pamene enzeli kukamba, Yudasi wina wao pali kumi na abiri, anabwela. Gulu likulu linabwela na eve kuchokela kubakulu bopeleka bansembe ndiponso bakulu ba banthu. banabwela na malupanga na vopumila. 48 Manje munthu wamene enzoyenekela kugulisa Yesu anabapasa chizibiso, ndikunena kuti, ''Aliyense wamene nizaposha nakutomola, ndiye wamene muzagwira.'' 49 Pameneapo anabwela kuli Yesu na kukamba ati, ''Mulibwanji, Baphunzisi!'' ndiponso anamutomola eve. 50 Yesu ananena kuli iye, ''Muzanga, chita vamene wabwela kuchita.'' Ndipo bana bwela, kufaka manja pali Yesu, ndiponso banamugwila. 51 Onani, umodzi pali bamene banali na Yesu anatambusula kwanja kwake, nakudonsa panga yake, ndiponso anakwapula kapolo wa akulu opeleka bansembe, ndiponso anajuba kwatu yake. 52 Koma Yesu ananena kuli eve, ''Faka panga mumalo yake, chifukwa aliense wamene apaya na lupanga azafa na lupanga. 53 Kodi uganizila kuti asembe sinaitanile Batate banga, asembe sibanitumila ma gulu ya angelo kupambana zikwi khumi na yabiri? 54 Koma nimunjila yabwanji yamene malemba yazafikilisiwamo, kuti izi zichitike?'' 55 Pali ija nthawi Yesu anauza gulu ati, ''Kodi mwabwela na mapanga na vopumilako nakunitenga monga ndine kawalala? Nenzonkhala lyonse mutempele na kupunzisa, ndiponso simunanimange. 56 Koma ivi vonse vachitika kuti malembo ya aneneri yafikilizike.'' Ndiponso bonse bophunzila banamusiya nakuyenda. 57 Baja bamene banamugwira Yesu banamupeleka kuli Kayafasi mukulu wa bansembe, kwamene bolemba na bakulu banakumana pamodzi. 58 Koma Petulo anamukonkha mosiyako kamalo kang'ono na nyumba ka mukulu wa bakulu bansembe. Anayenda mukati ndiponso anankhala pansi na bamalonda kuti aone vamene vizachokamo. 59 Manje mukulu wa opeleka nsembe ndiponso bonse bamukabungwe banali kuyanganila paukamboni waboza onamizila Yesu, kuti bamupayilepo. 60 Sibanapeze aliyense, chingankhale bakhamboni bambiri banabwela pasogolo. Koma pambuyo pake babiri banabwela pasogolo 61 ndiponso banakamba ati, '' Uyu mwamuna anakamba kuti, 'Ningakwanisa kuononga tempele ya Mulungu ndiponso nakuimangana futi muma siku yatatu.'' 62 Mukulu wabopeleka nsembe anayimilila no kamba kuli eve ati, ''Kodi ulibe yankho? Nanga nichani chamene bapasila umboni pali iwe?'' 63 Koma Yesu anankala zii. Mukulu wabopeleka bansembe anakamba ati, ''Nakulamilila iwe mwa Mulungu wa moyo, tiuze ngati ndiwe Kristu, Mwana wa Mulungu.'' 64 Yesu anamuyanka ati, ''Wakamba ivi wamene iwe. Koma nikuuzani imwe, kuchokela pano muzaona Mwana wa Munthu ankhala kuzanja lamanja la Mphamvu, ndiponso alikubwela pa makumbi ya ku mwamba." 65 Ndipo mukulu wa bopeleka bansembe anang'amba zovala zake ndi kunena kuti, ''Akamba manyozo! Nichani chamene tikalikusakilila bakamboni? Onani, manje mwamvela manyozo. 66 Muganizapo chani?" Banayankha no kamba ati, ''Ayenekela kufa.'' 67 Koma banabwela bamutunyila mata kumanso ndiponso kumumenya, ndikumukwapula na kanjeza kumanja yake, 68 ndiponso ananena, ''Nenelani kuliise, iwe Kristhu. Nanga ni ndani wamene enze kukukwapula?'' 69 Manje Petulo enze nkhale panja pa malo yanyumba, ndiponso wanchito mukazi anabwela kuli eve nakumuuza ati, ''Naiwe wenzeli na Yesu waku Galileyo.'' 70 Koma anakana pasogolo pabo bonse, nokamba, ''Siniziba vameneukambapo.'' 71 Pamene anayenda kunja kwanjila, wanchito wina anamuona ndiponso anauza baja benzepo ati, ''Uyu mwamuna naeve enzeli na Yesu waku Nazareti.'' 72 Nafuti anakana ndikulapa, ''Sinimuziba!'' 73 Pamene kunapita ka nthawi kang'ono baja bamene bana imilila pafupi banabwela nakumuuza Petulo ati, ''Zoona ndiwe wina wa amodzi aba, chifukwa makambidwe yako yakugulisa.'' 74 Koma anayamba kutembelela na kulapa, ''Sinimuziba uyu munthu,'' ndiponso pameneapo kombwe analila. 75 Petulo anakumbuka mau yamene Yesu anakamba, ''Pamene kombwe akalibe kulila uzanikana katatu.'' Ndiponso anayenda panja na kulila kuipa.