Mutu 25

1 "Ufumu wakumwamba uzakankala monga ba namwali bali kumi bamene banatenga tunyali twabo kuyenda kuti bakakumane naye okwatiliwa. 2 Basanu pali aba banali bopusa koma basanu benangu banali bochenjela. 3 Chifukwa pamene banamwali bopusa banatenga tunyali twabo, sibanatenge na mafuta yosebenzesa mu tu nyali twabo. 4 Koma banamwali bochenjela bana tenga tu gubu pamozi na tunyali twabo. 5 Manje pamene okwatiliwa anachedwa kufika, bamvela tulo naku gona. 6 Koma pa kati ka usiku kunali kupunda, 'Onani, okwatiliwa! Endani muka kumane na e. 7 Pamene apo bonse baja banamwali banaima naku yasha tu nyali twabo. 8 Baja bopusa bana uza bochenjela kuti, 'tipempako mafuta chifukwa tunyali twatu tuzazima.' 9 "Koma baja bochenjela banayanka kuti, 'Chifukwa siku zankala yokwanila kuti imwe naise tigabane, imwe endani kuli baja bamene bagulisa mukagule yanu yosebenzesa.' 10 Pamene bana enda kukagula, okwatiliwa anabwela, na bonse baja bamene banali bokonzekela bana enda na-e kupwando, bana koma nachiseko. 11 "Kuchoka apa manje baja banamwali benangu banabwela nakukamba kuti, 'Bwana, bwana, tisegulileni koni.' 12 "Koma anabayanka nakukamba kuti, 'Zoona nikuuzani imwe, ine sinikuzibani imwe.' 13 Onesesani, chifukwa imwe simuziba siku kapena ntawi. 14 "Chifukwa chili monga muntu wamene afuna kuenda kuziko ina. Anabaitana bantchito bake naku bapasa chuma chake. 15 Kuli umozi anapasa ndalama zisanu, kuli wina zibili, na kuli wina anapasa ndalama imozi. Ali onse analandila zokwanila monga mwamene angakwanilisile, na uja muntu ana enda pa ulendo wake. 16 Uja wamene analandila ndalama zisanu ana enda pamene apo naku zisebenzesa ndalama zija naku pangilapo ndalama zinangu zokwanila zisanu. 17 Chimozi-mozi uja wamene analandila ndalama zibili anapangilapo ndalama zinangun zibili. 18 Koma uja wantchito wamen eanalandila ndalama imozi ana enda, naku kumba mugodi, nakubisa ndalama za bwana wake. 19 Manje pamene panapita ntawi ikulu bwana wa baja bantchito anabwelela naku pendelana ndalama. 20 uja wantchito wamene analandila ndalama zisanu anabwela naku leta ndalama zinangu zisanu. Anakamba kuti, 'Bwana, imwe mwenze munanipasa ndalama zisanu. Onani, ninapangilapo ndalama zinangu zisanu.' 21 "Bwana wake anamu uza kuti, 'Wachita bwino, wantchito wabwino okululupilika! Unali okululupilika pa tuntu tungóno. Apa manje ine nizakupanga o onela vambili. Ngena mu chimwemwe cha bwana wako.' 22 "Wantchito uja wamene analandila ndalama zibili anabwela nakukamba kuti, 'Bwana, imwe munanipasa ndalama zibili. Onani, napangilapo ndalama zibili zinangu.' 23 Bwana wake anamu uza kuti, 'Wachita bwino, wantchito wabwino okulupililika! Unali okululupilika pali tuntu tungóno. Niza kuika olanganila vintu vambili. Ngena mu chimwemwe cha bwana wako.' 24 "Pamene apo wanchito uja wamene analandila ndalama imozi anabwela naku kamba kuti, 'Bwana, Niziba kuti imwe ndimwe bolimba mutima. Muma kolola pamene imwe simunashange, ku unjikisa pamene imwe simuna tayepo. 25 Ine ninali na manta, chifukwa chake ine nina enda naku bisa ndalama yanu pansi. Onani, tengani chintu chanu.' 26 "Koma bwana wake anamu yanka naku muuza kuti, 'Iwe wantchito oipa na ulesi, unaziba kuti ine nima kolola pamene sininashange naku unjikisa pamene sinina tayepo. 27 Iwe asembe una bwelekesa ndalama zanga kuli ba malonda ya ndalama, pakubwela kwanga asembe ninapeza ndalama zanga na za pamwamba. 28 Tengani ndalama ili kuli eve mupase uja wamene ali na ndalama kumi. 29 Chifukwa muntu ali onse wamene ali nazo, zambili zinangu zizapasiwa-zopitililapo. Koma uli uja wamene alibe kali konse, navija vamene ali navo azapokewa. 30 Mutayeni panja pamene pali mudima uyo wanchito wamene alibe pindu, pamene kuzankala kulila nakusheta meno.' 31 "Pamene Mwana wa Muntu azabwela mu ulemelelo wake na bangelo bonse pamozi na eve, pamene paja azakankala pa mupando wake waulemelelo. 32 Pa menso pake yonse maiko yazaka kumana, ndipo azakapatulula bantu wina kumuchosa kuli wina, monga mwamene mubusa ama patulula nkosa na mbuzi. 33 Azaika nkosa ku kwanja yake ya kwanja, koma mbuzi zizankala ku kwanja yake ya manzele. 34 Pamene apo Mfumu azakauza baja bamene bali ku kwanj ayake ya manja, 'Bwelani, imwe bamene munadalisika na ba Tate banga, tengani ufumu wamene banaku konzelani kuchokela pamene ziko inalengewa. 35 Chifukwa ine ninali na njala munanipasa bakudya; ninali na njta munanipasa chakumwa; Ninali mulendo munani landila munyumba zanu; 36 Ninali be vovala imwe munani valika; Ninali odwala imwe munanisamalila; Ninali mu ndende imwe munabwela kuniona.' 37 "Pamene apo baja bolungama bazakayanka nakukamba kuti, 'Ambuye, niliti pamene ise tinaku onani njala takusapani vakudya? Kapena na njota takupasani chakumwa? 38 Niliti pamene ise tinakuonani mulendo naku kulandilani? Kapena munalibe vovala nakuku valikani? 39 Niliti pamene tinaku onani kuti mudwala kapena mu ndende naku bwela kukuonani?' 40 "Pamene apo Mfumu izakayanka naku kamba kuli beve kuti, 'Zoona niku uzani imwe, chamene imwe muna chitila mungóno pali aba babale banga aba, munachitila ine.' 41 Aza kamba kuli baja bamene bali kukwanja yake ya manzele, 'Chokani apa, imwe botembelelewa, endani mu mulilo wamene unakonzekelewa mudani na bangelo bake, 42 chifukwa ine ninali na njala, koma simunani pase vakudya; Ninali na njota, koma imwe simunani pase chakumwa; 43 Nenze mulendo, koma imwe simunani landile mu manyumba yanu; ninalibe vovala, koma imwe simunani pase vovala; odwala na mu ndende, koma imwe simunani samalile.' 44 "Pamene apo baza kayanka nakukamba kuti, 'Ambuye, niliti pamene tenze tinakuonani na njala, kapena na njota, kapena mulendo, kapena osavala, kapena odwala, kapena mundende, ndipo ise siti naku tandizeni?' 45 "Azakayanka naku kamba kuti, 'Zoona nikuuzani imwe, vamene imwe simunachitile kuli mungóno pali umozi waba aba, simunachitile ine.' 46 Aba bazaka yenda muku kaulisiwa kwamene sikusila, koma balungami bazangena mu moyo wamene siusila."