MUTU 6

1 2 Manje chinabwela chachitika pa sabata kuti Yesu analikuyenda mumunda mwamene balima mbeu ndiponso bopunzila bake banali kudoba mitu zambeu, ndikuzinyanyaula mumanja yao ndiponso banalikudwa izi mbeu, Koma wina wa afalisi ananena, '' Kodi nichifukwa chachani chamene muchitila chinthu chamene sicholamulidwa kuchita pasikula sabata?'' 3 4 5 Ndiponso pakumuyankha iye, Yesu ananena, ''Kodi siunabelenge vamene David anachita pamene enze nanjala, Iye ndiponso nabamene analinabo? Anaenda munyumba ya Mulungu, nakutenga mukate wamene unali munso yake ndi kudyapo mbali yamukate, ndiponso anatengapo mukate wina nakupasa amuna bamene analinao kuti badye, angankhale chinali chabe chovomelezewa kuopeleka ansembe kudya.'' Ndiponso ananena kwaiyo, ''Kuti mwana wamuthu ni Mulungu wa sabata.'' 6 7 8 Chinachitika pa sabata inangu pamene anaenda musinagogi ndi kuuza banthu bena muja.Munali mwamuna muja wamene anali nazanjalamanja lolemala.Akalembela ndi afalisi analikumuyangana chabe pafupipafupi nakuona ngati azapolesa wina pasabata, pakuti bapezelepo chifukwa chomuzuzulilapo. Koma anaziba zamene banali kuganiza ndiponso ananena kuli mwamuna wamene kwanja yake inali yolemala, ''Anati ima, ndiponso uimilile pakati palialionse.'' Ndiponso mwamuna anaima ndiku imilila pamene paja. 9 10 11 Yesu ananena kwaiwo, ''Nikufunsa iwe, Kodi sicholamulidwa pasabata kuchita zabwino kuchila kuchita voipa, kupulumusa moyo kuchila kuuononga?'' Ndiponso anayanga baja bonse banamuzungulila ndikunena ku mwamuna, ''Tambusula kwanja yako.'' Anachita chomwecho, ndiponso kwanja kwake kunabwezewa. Ndiponso banazozedwa naukali ndiponso ananena kuliwina ndi muzaka chamene bangamuchite Yesu. 12 13 Chinabwela chachitika masiku yaja nichakuti anaenda kuluphiri kupempela. Anapitiliza kupempela kwa Mulungu usiku onse. Pamene kunali muzuba, anaitana opunzila bake, ndiponso anasankha kumi ndi tuwili bamene analikuitana ati maapostoli. 14 15 16 Mazina yama apostoli banali Simoni (wamene anainika ati Peter) ndiponso abale bake, Andeleo, Yakobu, Yoani, Philipo, Batilomeo, Mateyo, Tomasi, Yakobu mwana wa Alifas, Simon wamene anali kuitananiwa Ziloti, Judasi mwana wa Yakobu, Ndiponso Judasi Esikalyoti wamena anali ogulisa. 17 18 19 Koma Yesu anabwela pansi paluphiri ndi iwo nakuimilila pamalo pamene panali polingana ndi ophunzila bake bambiri ndiponso gulu ikulu yabathu baku Judeya ndiponso Jelusalemu ndiponso akuchimana chaku Tyre ndiponso Sidoni. Banabwela kumvelela kwaiye ndiponso kuchilisiwa kumatenda yao. Banthu bamene anavutisiwa ndi mizimu zonyansa anachilisiwa.Alionse mugulu analikuyeselela kumugwila chifukwa mphanvu zochilisa zinalikuchoka mwaiye, ndiponso anabachilisa bonse. 20 21 Ndiponso anayanganila paophunzila bake, ndi kunene, ''Ndimwe odala imweamene aliosauka, chifukwa ufumu wa Mulungu ndiye wanu. Ndimwe odala bamene mulinanjala, chifukwa muzazozedwa. Ndimwe odala imwe bamene mulila, chifukwa muzaseka. 22 23 Ndimwe odala ngati banthu banthu bakuzondani ndiponso kukupatulani ndiponso kukutukwanani, chifukwa chamwana wa munthu. Sekelelani muli ija siku ndiponso ndi chimwemwe, chifukwa muzankhala ndi mphatso yaikulu kuchoka kumwamba, ndi mibado yao inachita kuaneneli babo munjila imozimozi. 24 25 Koma vuto ilikuli imwe bamene olemela, chifukwa mwalandila kudala tontozo lanu. Vuto ilikuli imwe bamene aliokutila manje, chifukwa muzamvela njala pasogolo.ilikuli imwe bamene baseka manje, chifukwa muzalila malilo pasogolo 26 Vuto lili kwainu bamene banthu banena zabwino paliimwe, chikukwa iyo ndiye njila mwamene mibado yanu inivutisilamo ananeneli baboza. 27 28 Koma ninena kwainu bamene bamvela, kondani badani banu ndiponso mubachitile vabwino baja bamene bakuzondani.Dalitsani baja bamene bakutembelelani ndiponso mubapempelele baja bamene bakuvutisani. 29 30 Kuli iwo bamene bakumenyani kutobo, mupasenso ndi kwinakwache.Ngati munthu wina atenga koti yako, usagwilililenso chovala chako. Pasa aliyense wamene akupempa.Ngati munthu wina atenga chinthu chako, usamufunse kuti akubwezele. 31 32 33 34 Monga mwanene ufuna banthu bena kukuchitila, Naiwe uchite chimodzimodzi kulibemve. Ngati ukonda chabe baja bamene bakukonda, Kodi nipindu bwanji yamene ingankale kwaiwe? chifukwa ndi ochimwa akonda kuchita chimodzimodzi. Ngati ukongolesa chabe kuli banthu bamene uganizila kuti ndibemve bazakubwezelanso, Kodi nipindu bwanji iyo kuliiwe? Ndi ochimwa amakongolesa kuochimwa, kuti alandile mumuyeselo umodzi. 35 36 Koma kondani adani banu ndiponso bachitileni vabwino.Kongolesani koma musaganizile kulandila chilichonse ndiponso mphatso yanu izankhala yaikulu ndiponso muzankhala bana babapamwamba, chifukwa iye mwinewake niwabwino kulibaja banthu bamene sibayamika ndiponso kuli boipa. Nkalani bachifundo, monga mwamene tatewanu ali wachifundo. 37 Musaweluze , ndiponso simuzaweluzidwa, musasule, ndiponso naimwe simuzasuliwa. Kululukila benzanu ndiponso naimwe muzakululukidwa. 38 Pasani, ndiponso naimwe musapasidwa. mumueselo umodzi ndi chisangalalo_nakusindila pansi, ndiponso kuzisunkhani pamodzi ndiponso nakutaikila-zizatikila mumanja mwako.Koma mumuyeselo wamene muzasebenzesa, chizabwezedwa kwaiwe. 39 40 Ndiponso anabauza nthano, ''Kodi nanga munthu osaona angasogolele muzake wamene siaona? ngati angachiti, Ndiponso bonse bazagwela mumugodi, kodi simwamene?'' Ophunzila simukulu kupambana muphunzisi, koma alionse ngati afikapo pakuphunzisiwa azanhkala monga muphunzisi wake. 41 42 Ndiponso nichifukwa chani muyanganila pakanthu kang'ono kali mulinso lamubale wako, Koma iwe siunazindikila mutengo ukulu mulinsolako? Ungakambe bwanji kumubalewako, mubale, ' Lekanichose kanthu kang'ono mulinsolako; ngati iweweka siungaone chimutengo chikulu mulinsolako? Imwe onama! choyamba chosa chija chimutengo chikulu mulinsolako,ndiponso uzaona bwinobwino pakuti uchose kaja kumutengo kang'ono mulinso lamubale wako. 43 44 Koma kulibe chimutengo chabwino chamene chingabeleke zipaso zoola, angankale chimutengo choola chamene chingabeleke zipaso zabwino, Koma chimutengo chilichonse chizazibika kulinganiza nazipaso zamene chibeleka.Banthu sibama kolola visepo kuchimutengo chaminga zamusanga, angankhale kukolola magrepusi ku mabriya yamusanga. 45 Munthu wabwino kuchokela muchipao chaubwinowake wamumutima amabeleka za bwino, ndiponso munthu oyipa kuchokela muchipao chakuipa kwamumutima wake amabeleka zoipa. Koma kuchokela mu unyinji waza mumutima kamwa kazanena. 46 47 48 Nichifukwa chani chamene muniitanila, 'Ambuye, Ambuye,' ndiponso simumvelela zinthu zamene nikuuzani? Alionse wamene abwela kwaine ndiponso nakumvelela mau yanga, Nizakuuzani mwamene alili.Ali monga munthu wamene amanga nyumba, wamene anakumba pansi pantaka ndiponso nakumanga chi manyumba pamwala olimba.pamene kuziliwa kwamanzi kunabwela, kupopota kwamanzi kunachaya nyumba ija, koma siinagwedezeke, chifukwa yenze inamangiwa bwino. 49 Koma munthu wamene amvela mau, ndiponso siayamvelela, alimonga munthu wamene anamanga nyumba pamwamba pantaka kopanda chiyambi. pamene kupopota kwamanzi kunachaya munyumba, pamene apochabe inagwa, ndiponso chibadwile chaija nyumba chinasila.''