Mutu 4

1 Okondewa,osakululupira muzimu olionse,koma yesani mizimu zonse kuziba ngati ichokela kuli mulungu,cifukwa aneneli aboza agena muziko. 2 Pali ichi muzaziba muzimu wa mulungu-muzimu ulionse wamene uzavomela kuti Yesu Kristu anabwela mu munthu achokela kuli mulungu, 3 ndiponso muzimu alionse wamene siuvomela Yesu siuchokela kuli mulungu. Uyu nimuzimu osusana na kristu,wamene munanvela ati ubwela,ndiponso unabwela kudala. 4 Munachokela kuli mulungu, imwe bana,ndiponso munabagonjeza,cifukwa wamene alimuli iwe niopambana kuchila wamene alimu ziko. 5 Bachokela muziko, navamene bamakamba vichokela muziko,naziko imabanvelela. 6 Ise tichokela kuli Mulungu. Wamene aziba Mulungu amatinvelela. Wamene siachokela kuli Mulungu samatinvelela. Pali ichi tizaziba muzimu wachoonadi namu zimu waboza. 7 Bokondedwa,tiyeni tikondane,cifukwa chikondi chichokela kuli mulungu.Nabonse bana konda nibobadwa kuli mulungu ndiposo bamuziba mulungu. 8 Muntu wamene siamakonda siaziba mulungu,cifukwa mulungu ndiye chikondi. 9 Cifukwa chaichi chikondi cha mulungu chinavumbulisiwa pali ise,kuti mulungu anatuma mwana wake eka muziko pakuti tinkale cifukwa cha iye. 10 Umu mu chikondi,sikuti tinamukonda mulungu,koma anatikonda,ndiponso anatuma mwana wake kunkala otikambilako kuma chimo watu. 11 Bokondedwa,ngati mulungu anatikonda,naise tikondane. 12 Kulibe anaonapo mulungu. Ngati tikondana mulungu ankala muli ise. Nachikondi chake nichosilizika muli ise. 13 Pali ichi tiziba ati tinkalilila muli iye na iye muli ise,chifukwa anatipasako mbali mbali yamuzimu wake. 14 Ndiponso,tinaona ndikupelekela umboni kuti mulungu anatuma mwana wake kubwela kunkala mupulumusi wa ziko. 15 Aliyense wamene azavomela ati Yesu nimwana wa mulungu,mulungu azankala mulu iye. 16 Ndiponso taziba na khukululupira chikondi chamene mulungu alinacho pali ise. Mulungu nichikondi,nawemene ankala muli ichi chikondi ankala muli mulungu,ndiponso mulungu ankala muli iye. 17 Chifukwa chaichi,ichi chikondi chankala chosililizika pali ise,pakuti tikankale nachisindikizo pasiku yoweluza, monga mwamene alili,ndiye mwamene tilili muziko. 18 Kulibe manta muchikondi.malo mwa,chikondi chosilizika chimataya manta,chifukwa manta iyendelana na chilango. Koma wamene ayopa sanasilizike mu chikondi. 19 Timakonda chifukwa mulungu anatikonda pachiyambi. 20 Ngati alionse akamba,''Nikonda Mulungu,''koma siakonda mubale wake, niwaboza.koma wamene siakonda mubale wake, wamene siangakonde Mulungu wamene sianaone. 21 Ndiponso iyi ndiye lamulo yamene tilinayo kuchekela kwa iye: Wamene akonda Mulungu afunikanso kukonda mubale wake.