Mutu 5

1 Ndipo ninaona mumanja mwa iye amene anakhala pa mpando wa chimfumu ku dzanja la manja lake, chi buku cholembewa mbali zonse ziwiri. Inali yosindikiziwa na zosindikizira 7. 2 Ninaona mngelo wa mphamvu kukuwa ni mau okweza, "Ndani oyenera kusegula buku na zosindikizira zake?" 3 Palibe aliyense kumwamba, padziko la pansi kapena pansi pa dziko yemwe anali oyenera kusegula buku kapena kuwerenga. 4 Ninalira maningi chifukwa panalibe aliyense oyenera kusegula kapena kuwerenga buku. 5 Koma m'mozi wa akulu-akulu anati kwa ine, "Usalire. Ona! nkhalamu ya mtundu wa ayuda, muzu wa Davide, wapambana. Akwanisa kusegula buku na kusegula zosindikizira zake." 6 Ninaona mwana wa nkhosa kuimilira pakati pa mpando wa chimfumu na zamoyo zinai ndinso pakati pa akulu 24. Anaoneka monga anali ataphedwa. Anali na manyanga 7 na menso 7; Aya ni mizimu 7 ya Mulungu yotumizidwa ku dziko lonse lapansi. 7 Anapita ndi kukatenga buku lija ku dzanja la manja la yemwe akhala pa mpando wa chimfumu. 8 Pamene mwana wa nkhosa anatenga buku, za moyo zinai ndi akulu 24 anagwa pansi kumulambira. Aliyense anali na mtolilo na mbale yodzala ndi zinthu zonunkhira, yomwe ni ma pemphero ya okhulupilira. 9 Anaimba nyimbo ya sopano: Ndinu oyenera kutenga buku ndi kulisegula zosindikizira zake. Chifukwa munaphedwa, ndipo na magazi anu munagula anthu a mitundu yonse kwa atate, chilankhulo, mtundu, anthu na maiko. 10 Munawapanga ufumu, ndi ansembe kutumikira Mulungu wathu, ndipo azakhala pa dziko la pansi." 11 Ndipo ninaona ndi kumva mau ya angelo ambiri kuzungulira mpando wa chimfumu, zamoyo zinai ndi akulu 24. Unyinji wao unali zikwi ndi zikwi. 12 Ananena mu mau okweza, "Ndi oyenera mwana wa nkhosa yemwe anaphedwa kulandira mphamvu, ulemelero,nzeru, ulemu na matamando." 13 Ninamva cholengedwa chilichonse kumwamba, padziko la pansi, na pansi pa dziko la pansi ni mu manzi- zonse zopezekamo- kukamba ati, "kwa iye okhala pa mpando wa chimfumu na kwa mwana wa nkhosa, kukhale matamando, ulemu, ulemelero ndi mphamvu zolamulira nthawi zonse." 14 Zamoyo zinai zinati, "Amen!" ndipo akulu anazigwesa pansi ndi kulambira.