Mutu 4

1 Pambuyo pa izi zinthu ninayang'ana, ndipo ninaona chiseko choseguka kumwamba. Mau oyamba omwe ninamva omwe yamakamba na ine monga lipenga kukamba ati, "bwera kuno, ndipo nizakuuza zamene zizachitika pambuyo pa izi." 2 Pa nthawi imeneyi ninali mu mzimu, ndipo ninaona kunali mpando wa chimfumu ku mwamba, ndipo panali wina onkhalapo. 3 Wamene analipo amaoneka monga jasper na carnelian. Panali utawaleza kuzungulira pa mpando wa mfumu. Utawaleza unaoneka umaoneka monga mwala wa emerald. 4 Kuzugulira mpando panaliso mipando 24, ndipo amene anankhala pa mipando imeneyi ni banthu bakulu-bakulu, obvala zobavala zoyera, na ma kolona ya golide ku mutu yao. 5 Pa mpando wa chimfumu panachoka moto wa kaleza, kugunda na kung'anima kwa mphenzi. Nyale 7 zimayaka pasogolo pa mpando, nyale zomwe ni mizimu 7 ya Mulungu. 6 Pasogolo pa mpando panali msinje wa galasi, monga kirisito. Pakati pa mpando ndi kuzungulira panali zamoyo zinai, zamenso yambiri, kusogolo na kumbuyo. 7 Chamoyo choyamba chenze kuoneka monga nkhalamu, cha chiwiri chenze kuoneka monga mwana wa ng'ombe, cha chitatu monga pa menso pa munthu, ndipo cha namba 4 chinali kuoneka monga mbalani youluka. 8 Zamoyo zimenez chilichonse chinali na mapiko 6, yozula menso pansi na pamwamba. Usiku na muzuba sivileka kukamba ati, "Oyera, Oyera, Oyera ni Mulungu wa mphamvu zonse amene analiko, aliko, ndipo azankhalako." 9 Nthawi zonse pamene za moyo zipereka ulemelero, ulemu na matamando kwa amene ankhala pa mpando wa chimfumu, wamene ankhala kwa muyaya, 10 akulu 24 amazigwesa pansi kulambira iye amene ankhala pa mpando wa chimfumu. Bamagwada kwa iye amene ankhala muyaya, ndipo amaponya pansi ma kolona yao ku mpando, kukamba kuti, 11 "Ndinu oyenera, ambuye athu na Mulungu wathu, kulandira ulemu, ulemelero ndi mphamvu. Chifukwa munalenga zinthu zonse, ndipo mwa chifuniro chanu, zinankhalako ndipo zinalengewa."