Mutu 6

1 Ninaona pamene mwana wa nkhosa anasegula imozi mwa zosindikizira 7, ndipo ninamva cimozi mwa zamoyo zinai zija kukamba kuti mu mau amene anamveka monga mabingu, "Bwera!" 2 Ninaona ndipo panali kavalo oyera. Okwerapo ananyamula uta, ndipo anapasiwa kolona. Anachoka ngati opambana kuti apambane. 3 Pamene mwana wa nkhosa anasegula chosindikizira cha chiwiri, ninamvera chamoyo chachiwiri kukamba ati, "bwera!" 4 Ndipo kavalo anatuluka osweta. Wamene anakwerapo anapasidwa mphamvu yochosa mtendere pa dziko la pansi, kuti anthu aphane okha-okha. Okwerapo ameneyu anapasidwa chimpeni chachikulu. 5 Pamene mwana wa nkhosa anasegula chizindikiro cha chitatu, ninamvera chamoyo cha chitatu kukamba ati, "bwera!" ninaona kavalo wakuda, ndipo wamene anakwerapo ananyamula muyeso m'manja mwake. 6 Ninamvera mau yamene yanamveka kwati niya chimozi mwa zamoyo kukamba ati, "muyeso wa tiligu oguliwa dinari imodzi, ndi miyeso itatu ya balele yogulidwa dinari imozi. Koma osaononga mafuta na vinyo." 7 Pamene mwana wa nkhosa anasegula chizindikiro cha namba 4, ninamvera mau ya chamoyo cha chinai kukamba ati, "bwera!" 8 ndipo ninaona kavalo ombuwilira. Ndipo okwerapo dzina lake ni imfa, ndipo hade anali kulondola kumbuyo. Anapasidwa mphamvu ya gawo la dziko, kupha na chimpeni, njala na matenda na nyama za musanga za padziko. 9 Pamene mwana wa nkhosa anasegula chosindikizira cha namba 5, ninaona pansi pa guwa mizimu ya aja omwe anaphedwa chifukwa cha mau a Mulungu na umboni omwe anali nao. 10 Analira na mau okweza, "Mpaka liti, olamulira onse, oyera ndi wachoonadi, pomwe muzaweruza omwe ankhala pa dziko la pansi, pomwe muzabwezera magazi athu?" 11 Ndipo aliyense wa iwo anapasidwa mkanjo oyera, ndipo anauzidwa kuti ayembekeze pang'ono mpaka nambala ya akapolo anzao na bale ao ikwane omwe ayenera kuphedwa, monga momwe iwo anaphedwa. 12 Pamene mwana wa nkhosa anasegula chizindikiro cha namba 6, ninaona ndipo panali chibvomezi champhamvu. Dzuwa inada monga chovala chakutha ndipo mwezi unakhala monga magazi. 13 Nyenyezi za kumwamba zinagwa pansi, monga mwamene mtengo wa mkuyu umagwesera zipaso zake zosapya ngati mphepo yakuntha. 14 Kumwamba kunasoba monga buku lamene alupeteka. Mapiri na zitunda zinachosedwa pa malo ake. 15 Ndipo mamfumu na anthu olemekezeka, akulu a asilikali, olemera, amphamvu, ena onse, omasuka ni akapolo, anabisala mu mphanga na mu minyala ya m'mapiri. 16 Ananena kwa miyala na mapiri, "Tigweleni!" tibiseni ku nkhope ya iye amene ali pa mpando wa chimfumu ni ku mkwiyo wa mwana wa nkhosa. 17 Chifukwa siku la mphamvu la mkwiyo wao lafika. Ndani azakwanisa kuimilira?"