Mutu 9

1 Ndipo mngelo wa cisanu analiza lipenga yake. Ninaona nyenyezi kumwamba yamene inagwa pa dziko la pansi. Nyenyezi inapasiwa makiyi yosegulira mugodi opanda kolekezera. 2 Inasegula khomo la mugodi opanda kolekezera, ndipo panachoka utsi monga uchoka pa muliro waukulu. Dzuwa na mphepo zinadesedwa chifukwa cha utsi ochokera ku mugodi wamene uyu. 3 Kuchoka mu utsi dzombe unabwera pa dziko la pansi, ndipo inapasidwa mphamvu monga za kaliza pa dziko la pansi. 4 Yanauziwa kuti yasaononge mitengo kapena udzu pa dziko, koma chabe anthu amene alibe chizindikiro cha Mulungu pa mphumi pao. 5 Sibanapasidwe mphamvu zakupha anthu, koma kuwavutisa chabe kwa miyezi isanu. Ululu wake unali monga wa kaliza ngati waluma munthu. 6 Masiku ameneo anthu azafuna imfa, koma osaipeza. Azafuna maningi kuti afe, koma imfa izathaba. 7 Dzombe inaoneka monga kavalo okonzekera nkhondo. Pa mitu zao panali makolona agolide, ndipo nkhope zao zinali monga za munthu. 8 Anali na sisi monga mkazi, ndipo meno yanali monga ya nkhalamu. 9 Yanali na vobisa pa chifuwa monga va nsimbi, ndipo chongo chao chinali monga cha akavalo ambiri opita ku nkhondo. 10 Yanali na michila yolumila monga ya kaliza; ku michila yanali na mphamvu yoluma anthu kwa miyezi isanu. 11 Anali na wina monga mfumu pa iwo mngelo wa ku mugodi opanda kolekezera. Dzina lake mu chi heberi anali Abaddoni, ndipo mu chi greek anali na dzina lakuti Apollyon. 12 Soka loyamba lapita. Onani! pambuyo pa izi pali zilango zina zomwe zibwera. 13 Mngelo wa namba 6 analiza lipenga lake, ndipo ninamva mau ochokera mu nyanga ya pa guwa la golide yomwe ipezeka kwa Mulungu. 14 Liu linanena na mngelo wa nambala 6 yemwe anali na lipenga, "masula angelo anai omwe niomangiwa pa msinje waukulu wa Euphrates." 15 Angelo anai omwe anakonzedwera nthawi imenei, siku limeneli, mwezi umeneo na chaka chimenechi, anamasulidwa kuti aphe gawo lina la anthu. 16 Nambala ya anthu omwe anali pa msana wa akavalo ianali 200,000,000. Ninamva nambala yao. 17 Umu ni mwamene ninaonera akavalo mu masomphenya yanga na iwo okwerapo. Zovala pa zifuwa zao zinali zofiilira, zooneka bulumu ni zachikasu. Mitu ya akavalo imaoneka monga mitu ya nkhalamu, ndipo mkamwa mwao mumatuluka moto, utsi, na sufule. 18 Gawo lalikulu la anthu anafa chifukwa cha zilango zitatu zimenezi: Moto, utsi na sufule zomwe zinachoka mukamwa mwao. 19 Pakuti mphamvu ya akavalo inali mkamwa mwao na ku muchila kwao- chifukwa michila yao inali ngati njoka, ndipo inali na mitu yamene inali kupwetekera anthu. 20 Anthu ena onse, aja amene sanaphewe na zilango zimenezi, sanalape zoipa zamene anachita, kapena kuleka kupembeza ziwanda na mafano ya golide, siliva, bronze, minyala, na mitengo-zinthu zomwe sizipenya, kumva kapena kuyenda. 21 Sanalapenso pa kupha kwao, matsenga yao, chiwelewele chao kapena ncito zao za kuba.