Mutu 8

1 Pamene mwana wa nkhosa anasegula chizindikiro cha namba 7, kunali chete ku mwamba kwa theka la ola limozi. 2 Ndipo ninaona angelo 7 amene ankhala pa mpando wa chimfumu wa Mulungu, ndipo malipenga 7 yanapasidwa kwa iwo. 3 Mngelo wina anabwera, ananyamula mbale ya golide ya zonunkhirisa, kuimilira pa guwa la zonunkhirisa. Zonunkhirisa zambiri zinapasidwa kwa iye kuti apereke pamozi na mapemphero ya okhulupilira pa guwa la zonunkhirisa pa mpando wa chimfumu. 4 Utsi wa zonunkhirisa, na mapemphero ya okhulupirira, yanafikira ku mpando wa Mulungu kuchoka ku manja ya mngelo. 5 Mngelo anatenga mbale ya zonunkhira na kuikamo moto wa pa guwa. Ndipo anaiponya pansi pa dziko la pansi, ndipo panali phokoso la kaleza, kugunda na kung'anipa kwa mphenzi, na chibvomezi. 6 Angelo 7 omwe anali na malipenga anakonzeka kuti alize. 7 Mngelo oyamba analiza lipenga lake, ndipo panali mvula ya mphepo, moto yosakaniza na magazi. Inaponyedwa pa dziko la pansi kwakuti gawo lina linatenthedwa, gawo la mitengo inapya, ndi udzu onse obiliwira unapya. 8 Mngelo wa chiwiri analiza lipenga lake, ndipo chinthu china chachikulu monga phiri chinaponyedwa mnyanja. Gawo lina la manzi inankhala magazi, 9 zina mwa nyama za m'manzi zinafa, ndipo ma bwato ambiri anaonongeka. 10 Mngelo wachitatu analiza lipenga lake, ndipo nyenyezi yaikulu inagwa kuchoka ku mwamba, yoyaka monga tochi, pa gawo lalikulu la misinje na nyenje za madzi. 11 Dzina la nyenyezi ni chobaba. Ndipo madzi yanankhala yobaba, ndipo anthu ambiri anafa chifukwa cha manzi yobaba. 12 Mngelo wa chinai analiza lipenga lake, ndipo gawo lina la dzuwa linakanthiwa, ndi gawo lina la mwezi na gawo lina la nyenyezi. Sono magawo ambiri anadesedwa; gawo lina la siku na gawo lina la usiku linalibe kuwala. 13 Ninaona, ndipo ninamva mphungu yomwe imauluka pakati pa mitambo, kuitana na mau yokweza, "tsoka, tsoka, tsoka, kwa amene ankhala pa dziko la pansi, chifukwa cha malipenga omwe asalira kuti alizidwe na angelo atatu."