Mutu 7

1 Pambuyo pa izi ninaona angelo anai oimilira pa makona anai a dziko, kubweza mwa mphamvu mphepo zinai za dziko kuti mphepo iliyonse isathire pa dziko la pansi, pa nyanja, kapena pa mtengo ulionse. 2 Ni naona mngelo wina kuchokera ku m'mawa, amene anali na chizindikiro cha Mulungu wa moyo. Analira mokweza kwa angelo anai aja omwe anapasidwa mphamvu yoononga dziko la pansi na nyanja: 3 "Osaononga dziko la pansi, nyanja ndi mitengo mpaka pamene tizaika zizindikiro pa mphumi pa akapolo a Mulungu." 4 Ninamva nambala ya anthu amene anaikidwa zizindikiro: 144,000, omwe anaikidwa chizindikiro kuchoka ku mtundu ulionse wa anthu a Israel: 5 12,000 ochokera mju mtundu wa yuda anaikidwa zizindikiro, 12,000 kuchoka ku mtundu wa Reuben, 12,000 kuchoka ku mtundu wa Gad, 6 12,000 kuchoka ku mtundu Asher, 12,000 kuchoka ku mtundu wa Naphtaly, 12,000 kuchoka ku mtundu wa Manasseh. 7 12,000 kuchoka ku mtundu wa Simeon, 12,000 kuchoka ku mtundu wa L evi, 12,000 kuchoka ku mtundu wa Isaacher, 8 12,000 kuchoka ku mtundu wa Zebulun, 12,000 kuchoka ku mtundu wa Yosefe ndipo 12,000 kuchoka ku mtundu wa Benjamin analandira zizindikiro. 9 Pambuyo pa zinthu izi ninaona, ndipo panali anthu ambiri amene palibe angawerenge-kuchoka ku maiko onse, mtundu, anthu na chilankhulo-kuimilira pa mpando wa chimfumu ni mwana wa nkhosa. Anali atamvala zobvala zoyera, ndipo ananyamula nthambi za kanjeza m'manja mwao, 10 ndipo anali kukamba na mau okweza: " Chipulumuso chichokera kwa Mulungu wathu amene ankhala pa mpando wa chimfumu ni kwa mwana wa nkhosa!" 11 Angelo onse anali oimilira kuzungulira mpando wa chimfumu na kuzungulira akulu komanso zamoyo zinai, ndipo anagwa pansi kuyang'ana nkhope zao pansi kulambira pa mpando wa chimfumu. Anapembeza Mulungu, 12 kukamba kuti, "Amen! matamando, ulemelero, nzeru, mayamiko, ulemu, mphamvu, zinkhale kwa Mulungu nthawi zonse! Amen!" 13 M'modzi wa akulu ananifunsa ine kuti, "ndani awa, omwe abvala mikanjo yoyera, ndipo achokera kuti?" 14 Ninakamba nayeve kuti, "bwana, mudziwa" ndipo anati kwa ine, "Awa ndi anthu amene anachoka mu manzunzo yowawa. Awasha mikanjo yao na kuyayeretsa na magazi ya mwana wa nkhosa. 15 Pa chifukwa ichi, ali pa maso pa mpando wa Mulungu, ndipo amiupembeza usana na usiku mu nyumba yake. Iye wamene ankhalaa pa mpando wa chimfumu azaika tenti yake pa iwo. 16 Sazamveranso njala, kapena kumvera ludzu. Dzuwa sizawagwesa, kapena kutenthewa. 17 Chifukwa mwana wa nkhosa pakati pa mpando azankhala mbusa wao, ndipo azawapereka ku malo a manzi ya moyo, ndipo Mulungu azapukuta misozi mu menso yao."