Mutu 10

1 Pamene apo ninaona m'ngelo wina wamphamvu aseluka kucokela ku mwamba. Anavimbiwa na mukumbi, panali futi na uta wa leza pa mwamba pa mutu wake. Cinso cake cinali ngati zuba na mapazi yake yenze monga vipilala va mulilo. 2 Anali naka buku kakang'ono mu manja yake yamene yinali yosegula, na kuika kwendo la ku kwanja la manja pa cimumana na yakumanzele pa mtunda. 3 Pamene apo anapunda namau yopundisa monga ku uluma kwa mkango. Pamene anapunda, zo gunda 7 vinakamba nakuuluma kwake. 4 Pamene vogunda 7 vinakamba, nenze pafupi na kulemba, koma ninamvela mau kucokela ku mwamba yakunena, "Sunga nkama ya vimene vogunda 7 vanena. Usavilembe." 5 pamene apo mngelo amene nenze naona kuimilila pa mmana na pa calo, ananyamula kwanja lake lamanja ku mwamba. 6 Analumbila pa yeve ankala na moyo nthawi yonse, amene anapanga mumwamba na vonse vili mwa mene umo, calo na vonse vili mwa mene, na cimumana na vonse vili mwamene, na mngelo anakamba, "Sikuzankhala futi kucedwa. 7 Koma pa siku yamene mngelo wa 7 ali pafupi na kuliza mtolilo, pamene apo codadwisa ca Mulungu cizakwanilisika, monga mwamene ananena ku ba nchito bake maporofita." 8 Mau ninamvera kucokela ku mwamba yanalankhulanso kuli ine: "Pita, tenga buku losegula imene ili mu kwanja ya mngelo woimilila pa mumana na pa ziko." 9 Pamene apo ninayenda ku mungelo nakumuuza kuti anipase ka buku kakang'ono. Anakamba na ine, "Tenga buku na kudya. Izapanga mmala mwako ku baba, koma mkamwa mwako izankala yonzuna ngati uci." 10 Nina tenga kabuku kakang'ono kucoka ku manja a mngelo na kudya. Inali yonzuna monga uci mukamwa mwanga, nitasiliza kudya, mumala mwanga munababa. 11 Pamene apo wina anakamba na ine, ukambenso za anthu ambili, mitundu, malilime na mamfumu."