Chapita 11

1 Pamene Jabini, mfumu yaku Hazor, anameela izi, anatuma uthenga kuli Jobab, mfumu yaku Madori, kuli mfumu yaku Shimron, nakuli Mfumu yaku Akshaph. 2 Anatumansu uthenga kufuma yanali kumapili ya ku Mpoto kwaziko, mumana wa Yolodani kumwela kwa kinnereth, muzidikha, nakumitunda ya Dolo ku mazulo. 3 Anatumanso uthenga Akanani kumaa na ku ma zulo, ba Amoni, ba Hittites, ba Aperizi, ba Ayebusi mupili ya ziko, na ba Hivitesi pa phili ya Hermon mu ziko ya Mizpah. 4 Bonse bankhondo bao banacoka nabo, nambala ya ikulu yabasilikali, mu nambala monga dothi ya mumbali ya nyunja. Banali na nambala yaikulu ya akavalo na magaleta. 5 Yonse mafumu aya yanakumana panthawi yake, na kumanga pa manzi ya meloni kumenya nkhondo na Israyeli. 6 Yehova anakamba kuli Yoswa, ''Osayopa pamenso yabo, cifukwa mailo panthawi iyi nibapasa bonse kuli Israyeli monga banthu bakufa. 7 Yoswa nabonse bamuna bankhondo banabwela. Banafika mwazizizi pamanzi ya meroni, nakumenya mudani. 8 Yehova anapasa mudani mumanja ya Israyeli, anabakantha nakuba pepekela kusidoni, misrephoth maim, na ku cigwa ca mizpah ku mawa. banabakantha pakana kulibe apulumuka vmozi anasala. 9 Yoswa anacita kuli beve monga Yehova anabavzila. Anadula akavalo na kushoka magaleta. 10 Yoswa anabwelela panthawi ija nakutenga Hazor. Anakantha mfumu yabo napanga. (Hazor ndiye anali mkulu wa mizi izi). 11 Banakantha napanga ciliconse camoyo cinali muja, nakuvipatula kuti bavi bononge, ndipo kulibe ciliconse camoyo cinasiyiwa camoyo. Pamenepo anashoka Hazor. 12 Yoswa anatenga mizinda yonse ya mafumu aya anatenganso mafumu yabo nakuya kanth napanga ya kutwa. Anaba bonogelatu napanga yakutwa, monga mwamene Mose mtumiki wa Yehova analamulila. 13 Israyeli sanashoke mizinda ili yonse yomangiwa pa zitunda, kucosaka Hazor. Yekha cabe anashoka. 14 Bankhondo ba Israyeli banatenga vonse votenga mizi pamozi na vobeta. Banapaya munthu alibonse napanga yakutwa pakana onse banafa sibanasiye nyama yamoyo yopema. 15 Monga mwamene Yehova analamulila mutumiki wake Mose, munjila imozi, Mose analamulila Yoswa, na Yoswa anacita, sanasiyeko kalikonse kosacita ka mene Yehova analamulila Mose kucita. 16 Yoswa anatenga malo yonse: mapili yaziko, kumwela, malo yonse yau Gosheni, na ku madimba, mucigwa ca Yolodani, mapili ya ku Israyeli na ku madimba. 17 Kocokela kupili ya Halak pafupi na Edom, kupita ku mpoto kutali ku Gad mucigwa pafupi na Lebanoni pansi papili ya Hermoni, anatenga mafumu yonse na kubapaya. 18 Yoswa anamenya nkhondo kwanthawi itali na mafumu yonse. 19 Palibe muzinda umuzi unapanga mtendele na ba nkhondo ba Israyeli kucoselako ba Hivitesi banakhala mu Gibeori. Israyeli anatenga mizinda yonse munkhondo. 20 Popeza ni Yehova anakosesa mitima yabo kuti bamenya nkhondo na Israyeli, kuti aba bonongeletu popanda cifundo, monga mwamene anapasila malamulo Mose. 21 Ndipo Yoswa anabwela panthawi ija nakubononga ba Anakimu. Anacita izi mupili yaziko pa Hebroni, Debir, Anab, na mupili ya Yuda, na mapi yaziko ya Israyeli. Yoswa anababonongelatu pamozi namizinda yabo. 22 Kulibe waba Anakimu anasiwa mumalo ya ya Israyeli kucosako pa Gaza, Gath na Ashdod. 23 Pamene Yoswa anatenga malo, monga mwamene Yehova anakambila kuli Mose. Yoswa anapasa Israyeli monga cabo, Kupasiwa kumutundu vlibonse wao. Ndipo ziko inapumula kunkhondo.