Mutu 5

1 Iyi ndiye mbili ya bobadwa kwa Adamu pasiku lamene Mulungu anapanga mutundu wa anabapanga bolingana naye. 2 Mwamuna na mukazi anabapanga. Anabadalisa nakuba pasa zina kuti bantu pamene anabapanga. 3 Pamene Adamu anankhala zaka 130, anankhala tate wamwana mwamuna olingana naye, namaonekedwe yake, anamupasa zina Seti. 4 Pamene Adamu anankhala tate wa Seti, anankhala zaka 800. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 5 Adamu anankhala zaka 930 nakumwalila. 6 Pamene Seti anankhala zaka 105, anankhala tate wa Enoshi. 7 Pambuyo pake anankhala tate wa Enoshi, anankhala zaka 807 na kunkhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 8 Seti anankhala zaka 912, ndipo anamwalila. 9 Pamene Enoshi anankhala zaka 90, anankhala tate wa Kenani. 10 Pambuyo pake anankhala tate wa Kenani, Enoshi anankhala zaka 815. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 11 Enoshi anankhala zaka 905, ndipo anamwalila. 12 Pamene Kenani anankhala zaka 70, anankhala tate wa Mahalaleli. 13 Pambuyo pake anankhala tate wa Mahalaleli, Kenani anankhala zaka 840. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 14 Kenani anankhala zaka 910, ndipo anamwalila. 15 Pamene Mahalaleli anankhala zaka 65, anankhala tate wa Jaredi. 16 Pambuyo pake anankhala tate wa Jaredi, Mahalaleli anankhala zaka 830. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 17 Mahalaleli anankhala 895, ndipo anamwalila. 18 Pamene Jaredi anankhala zaka 162, anankhala tate wa Enoke. 19 Pambuyo pake anankhala tate wa Enoke, pamene anankhala tatea Enoke, Jaredi anankala zaka 800. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 20 Jaredi anankhala zaka 962, ndipo anamwalila. 21 Pamene Enocki anankhala zaka 65, anankhala tate wa Methuselah. 22 Enoki anayenda na mulungu zaka 300, pambuyo pake anankhala tate wa Methuselah. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 23 Enoki anankhala zaka 365. 24 Enoki anayenda na mulungu, ndiponso anasoba, chifukwa mulungu anamutenga. 25 Pamene Methuselah anankhala zaka 187, anankhala tate wa Lameki. 26 Pambuyo pake anankhala tate wa lameki, Methusela anankhala zaka 782. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 27 Methuselah anankhala zaka 969. Ndipo anamwalila. 28 Pamene Lameki anankhala zaka 182, anankhala tate wa mwana mwamuna. 29 Anamupasa zina Noah, nokamba kuti " Uyu azatipasa kupumula kunchito zantu na kubaba kwa nchito za manja, zamene tifunika kuchita chifukwa cha ntaka wamene yehova anatembelela." 30 Lameki anankhala zaka 595 pamene anankhala tate wa Noah. Anankhala tate wa bana bambili bamuna na bakazi. 31 Lameki anankhala zaka 777. Ndiponso anamwalila. 32 Pambuyo pake Noah anankhala zaka 500, anankhala tate wa Shem, Ham, ndi Japheth.