Mutu 6

1 Zinacitika izi pamene anthu anayamba kupaka pa ziko lonse na bana banakazi anabadwa kwa iwo. 2 Bana amuna a mulungu anaona bana banakazi ba anthu kuwama. Ndipo anabakwatira kunkhala akaazi awo aliyense anasankhapo wake. 3 Yahova anati, " Mzimu wanga suzapitiliza kulimbana na munthu nthawi yonse, cifukwa iye ali munthu. Moyo wake azakala zaka izo." 4 Vimbinga vinali pa calo pa masiku yaja, ndi pambuyo pake. Izi zinacitika pamene bana ba muna ba mulungu anakwatila bana ba kazi ba anthu ndipo bana balilana bana. Amena anali vimbinga panthawi ija ya kale ndi zomveka. 5 Yawe anaona kuti kuyipa mtima kwa munthhu kuli kukula pa ziko, ndipo maganizo yao ya mitima yao yanali yoipilathu nthawi zonse. 6 Yahova cinamubaba kuti anapanga munthu pa ziko, ndipo anamvela kuipa mumutima wake. 7 Ndipo Yehova ananena, " Nizacosapo mtundu wa anthu wamene ndina mpanga ine pa calo ca pansi - mtundu wa anthu ndi nyama, ndi zokalaba zonse ndi tunyoni twamwamba, cifukwa nimvela kuipa kuti ninampanga izi." 8 Koma Nowah anapeza mwayi pamaso pa Yehova. 9 Izi ndiye zamena zinacitika kwa Nowah. Nowah analiye munthu wolungama, ndipo pakati pa anthu analibe ili yonse pa nthuwi yake. 10 Nowa annayenda na Mulungu. Nowa anakhalatate wa bana bamuna batatu: Shemu, Hamu ndi Jafeti. 11 Ziko linaipa pa meso ya Mulungu ndipo inali yozula na ciwawa. 12 Mulungu danaona ziko; Onani, Inali yoipa kwamnbili cifukwa muntu aliyense woipa mujila yonse ya ziko. 13 Mulungu anakamba na Nowa, " Naona kuti yakwana nthuwi, kuti nicosepo munthu wonnse cifukwa calo cazola na ciwawa vicitika mwa iye, Zoonadi, Nizabaononga pamozi ndi ziko. 14 Koma kuli iwe upange chombo kucokela kuci mtengo ca kipulesi. Upange zipinda mu chombo ndi kuyanzikapo coletsa manzi kungena mkati na kunja. 15 Umu ndiye mwamena uzapangila: Kutalimpa kwa chombo ikale mikonoila 300, kufupika kwake mikono ili 50, ndikutalimpa mikono 30. 16 Upange mtenge wa chombo ndi usilize ndi mkono umodzi kuyambila pa mwamba pa cipuna. Uyikipo ciseko kumbali kwa chombo ndipo upange capansi, cacibili ndi cacitatiu cogonapo. 17 Nvela nili pafupi nakubwelesa cigumula ca manzi yambili pa ziko, kuonanga vintu vonse vamoyo va pa ziko. vonse pa ziko vizamwalila. 18 Koma nizanga chipangano na iwe uzabwela mu chombo, iwe na bana bako bamuna, na mukazi wako, na bakazi ba bana bako bamuna. 19 Ndi zolengendwa zonse zamoyo zibili zibili uzibwelese mu chombo, zimuna na zikazi, zinkale na umoyo na iwe. 20 Vinyoni kulingana na mtundu wake, pa nyama kulingana ndi mtundu wake, pa zokalaba za pa dothi kulingana ndi mtundu wake, zibili zosi yana zizabwela kuli iwe kuzisunga namoyo. 21 ika pamozi vakudya vosiyala ndipo usunge kuti vikhale vakudya na vao." 22 Ndipo Nowa anacita izi. Kulingana na vonse vamena Mulungu anamulamulila, ndipo anacita.