Mutu 41

1 Pamene panapita zaka zokwananila zibili zatuntulu, Farao analota. 2 Onani, anaimilira mumbali mwa Nailo. Ndipo, onani, ng'ombe zisanu na zibili zinachoka mumumana wa Nailo, zabwino ndipo zoina futi, ndipo zinali kudya muma bango. 3 Onani, ng'ombe zina zokwanila zisanu na zibili zinabwela kukonkapo kuchoka mu Nailo, zoyonda zosaoneka bwino. Beve banaimilila pafupi na ng'ombe zina mumpepete mwa mumana uja. 4 Ndipo ng'ombe zosaoneka bwino zija zoyonda zinadya ng'ombe zisanu ndi ziwiri zija zabwino zoina. Pamene apo Farao anauka. 5 Anagona futi ndipo analota nafuti kachibili. Onani, ngala zisanu na zibili za tirigu zinamera pa phesi imodzi, zabwino na zabwino. 6 Ndipo onani, ngala zisanu na zibili, zofota zo ochewa na mpepo ya kum'mawa, zinamela pambuyo pawo. 7 Mitu yofota inamela ngala zisanu ndi ziwili zija zabwino koma futi zozula. Pamene Farao anauka, onani, yanali chabe maloto. 8 Ndipo kuseniseni muzimu wake unavutika maningi. Anatumiza kukaitana bamasenga pamozi na banzelu bonse ba ku Aigupto. Farao anabawuza beve maloto yake, koma panalibe wamene anakwanisa kumumangusulila Falao. 9 Pamene apo mukulu wa bopelekela chiko anakamba kuli Farao kuti, "Lelo niganizila oa volakwa vanga. 10 Farao anakalipa na banchito bake, ndipo anani ponya mundende munyumba ya mukulu wa bolonda, ine na mukulu wa bopika buledi. 11 Usiku wamene uja, eve na ine tinalota ali onse kulingana na tantauzo ya maloto yake. 12 Kwamene kuja tinali pamozi na munyamata wina wachi Heberi, wanchito wa mukulu wa basilikali bolondela mfumu. Tina muuza ndipo anati masulira maloto yatu. Anamasulira ali onse wa pali ise maloto yake. 13 Vinachitika monga mwamene anatimangusulira, ndipo vinachiti. Farao ananibweza panchito yanga, koma winangu uja anapachikiwa. " 14 Pamene apo Farao anatumiza nakumuitana Yosefe. Beve banachita mwa mwachangu naku muchosa mu'ndende muja. Ndipo anagela sisi, nakuchinja vovala, nakungena mwa Farao. 15 Farao anakamba na Yosefe kuti, Ine ninalota, koma palibe wamene angani mangusulire maloto yanga; koma namvela va iwe, kuti ukamvela chiloto, ukwanisa kumangusula. 16 Yosefe anamuyanka Farao, kuti, "Sichilii mwa mwa ine. Mulungu azayanka Farao mwadaliso." 17 Farao ankamba na Yosefe kuti, "Mukulota kwanga ine, onani, ninaimilila mumbali mwa mumana wa Nailo. 18 Onani, ng'ombe zisanu na zibili zinachoka mumumana wa Nailo, zoina zooneka bwino, ndipo zinadya pakati pa mabango. 19 Onani, ng'ombe zinangu zinabwela zokonkapo, zofoka, zosaoneka bwino, zoyonda. Ine sininaonepo muziko yonse ya Aigupto zosaoneka bwino monga zija. 20 Ng'ombe zoyonda zosaoneka bwino zija zinadya ng'ombe zisanu ndi ziwiri zoyambilila zoina. 21 Pamene zinazidya zija, sizinazibike kuti zinadya, chifukwa zinali zosaoneka bwino monga poyamba. Pamene apo ninauka. 22 Ninayang'ana chiloto changa, onani, ngala zisanu na ziwiri zinamela pa pesi imozi, zozula koma futi zabwino. 23 Ndipo ona, ngala zina zisanu na zibili, zofota, zoyonda, zoochewa na na mpepo ya kum'mawa, zinamera pambuyo pabo. 24 Ngala zoyonda zija zinamela ngala zisanu ndi ziwiri zabwino zija. Ninauza bamasenga baja, koma panalibe wamene anakwanilisa kunimangusulila ine." 25 Yosefe anakamba kluli Farao kuti, "Maloto ya Farao ni yolingana. Chamene Mulungu afuna kuchita achilangiza kuli Farao. 26 Ng'ombe zisanu na zibili zabwino zija ni zaka zisanu na zibiri, ndipo mitu isanu na ibili yabwino ni zaka zisanu na zibiri. Maloto ayo ni yolingana. 27 Ng'ombe zikazi zisanu na zibili zoyonda zosakondewa zamene zinamela pambuyo pawo ndiye zaka zisanu ndi zibili, ndipo ngala zisanu na zibiri zoyonda zoochewa na mphepo ya kum'maŵa zizakala zaka zisanu na zibili za njala. 28 Ichi ndiye chintu chamene ninakamba kuli Farao. Vamene Mulungu afuna kuchita amu langiza Farao. 29 Onani, zaka zisanu na zibili zo chulukila zizabwela mudziko yonse ya Aigupto. 30 Zaka zisanu na zibili za njala zizafika pambuyo pako, ndipo zochuluka zonse zizaka ibalika m'dziko ya Aigupto, ndipo njala izaononga ziko. 31 Vochulukila iva sivzazakumbukiliwa muziko chifukwa cha njala yamene izakonkapo, chifukwa izakankala yoyofya kwambili. 32 Chamene chiloto ichi chabwezelewapo kuli Farao nichifukwa chakuti nkani yamene yi yankazikisiwa na Mulungu, ndipo Mulungu azachichita posachedwa. 33 Manje lekani Farao afunefune muntu wozindikila koma futi wanzeru, amunkazikise eve kunkala olanganila dziko ya Aigupto. 34 Lekani Farao aike boyanganila ziko, ndipo atenge imodzi pa magawo yasanu ya zokolola za mu Aigupto muzaka zisanu ndi zibili zokolola vochulukila. 35 Basonkanise vakudya vonse va zaka vabwino vamene vizabwela ndipo basunge tirigu mumanja ya Farao, inkale yakudya mumi zinda. Bayenera kusunga. 36 Chakudya chamene ichi chizankala chakudya chamu ziko mokwanila zaka 7 za njala yamene izankale muziko ya Iguputo. Munjila yamene iyi ziko si izawonongewa na njala." 37 Magangizo yamene aya yanali yabwino kuli Farao na kuli banthito bake bonse. 38 Farao anakamba kuli banchito bake kuti, "Nanga tingapeze muntu wamene ali monga uyu, wamene muli Mzimu wa Mulungu?" 39 Ndipo Farao anakamba kuli Yosefe kuti, "Popeza kuti Mulungu akuwonesa iwe ivi vonse, palibe winangu wamene niwozindikila nafuti wanzelu monga iwe. 40 Iwe uzankala woyanganila nyumba yanga, ndipo monga mwa mawu yako banthu banga bonse bazalamuliwa. Nizankala mkulu kuchila iwe pamupando chabe." 41 Farao anakamba kuli Yosefe kuti, "Ona, nakunkazika iwe woyanganira ziko yonse ya Igupto." 42 Farao anavula mphete yake yozindikizila kumanja kwake nakuivalika pa kwanja ya Yosefe. Anamuvalika futi vovala va nyula yabwino maningi, ndipo anamumanga na cheni ya golide mumukosi mwake. 43 Anamuyendesela mu galeta yachibili yamene anali nayo. Amuna banamu pundila pasogolo pake, "Gwadani pansi." Farao anamuika kunkala woyanganila ziko yonse ya Igupto. 44 Farao anakamba kuli Yosefe kuti, "Ine ndine Farao, ndipo kuchoselako iwe, palibe muntu wamene azatambasula kwanja yake kapena kwendo yake yake mu ziko yonse ya Igupto." 45 Farao anaitana Yosefe zina yakuti "Zapenati-Paniya." Anamupasa Asenati, mwana wamukazi wa Potifera wansembe waku Oni, kuti ankale mukazi wake. Yosefe anayenda-yenda mu ziko ya Igupto. 46 Yosefe anali wa zaka makumi yatatu pamene anaimirira pamaso pa Farao, mfumu ya Igupto. Ndipo Yosefe anachoka pamenso pa Farao, naku yenda yenda mu ziko yonse ya Igupto. 47 Muzaka zisanu na zibili mwa vochulukila va mu ziko ija vinapakisa mochilapo. 48 Anasonkanisa vakudya vonse va zaka zisanu na zibili vamene vinali muziko ya Igupto nakusungila vakudya vamene ivi mumizinda. Eve anaika vakudya mumizinda zamene zinali pafupi naminda zamene zinali mumbali mwake. 49 Yosefe anasunga tirigu monga muchenga wa kumanzi, kufikila mpaka anasiya kupendela, chifukwa vinali vinapakisa kwambili mosakwanisika kupendewa. 50 Yosefe anali na bana bamuna zaka zibili za njala ikalibe kufika, wamene Asenati mwana wamukazi wa Potifera wansembe waku Oni anamubelekela eve. 51 Yosefe anapasa zina mwana wake woyamba Manase, chifukwa anakamba kuti, "Mulungu andi ibalisa mavuto yanga yonse na banja yanga yonse ya batate banga." 52 Anapasa zina ya mwana wake wachibili Efulemu, chifukwa anakamba kuti, "Mulungu anibalisa mu ziko ya vovutisa vanga." 53 Zaka zisanu na zibili za vakudya vambili vamene vinali mu ziko ya Igupto inasila. 54 Zaka zisanu na zibili za njala zinayamba, monga mwamene anakambila Yosefe. Kunali njala muma ziko yonse, koma muziko yonse ya Igupto munali vakudya. 55 Pamene ziko yonse ya Igupto inali na njala, banthu banaitana kuli kuli Farao kuti abapase vakudya. Ndipo Farao anakamba kuli ba Igupto bonse kuti, Endani kuli Yosefe mukachite vamene eve akamba. 56 Njala inali paliponse paziko yapansi. Yosefe anasegula nkokwe zonse nakugulisa kuli bantu baku Igupto. Njala inakula maningi muziko ya Iguputo. 57 Dziko yonse inali kubwela ku Iguputo kugula tirigu kuli Yosefe, chifukwa njala ija inali inafika poipa kwambili paziko yonse yapansi.