Mutu 40

1 Zinabwela pambuyo patapita ivi vintu, wopelekela chakumwa kwa mfumu ya ku Igupto ndi wopanga buledi anakalipisa bwana wawo, mfumu ya ku Igupto. 2 Farao anakalipila banchito bake bakulu bakulu babili, mukulu opeleka chakumwa na mukulu bopanga buledi. 3 Anabaika mu jele mu nyumba ya malonda mukulu, mu jele mwamene Yosefe analili. 4 Mukulu wa bamalonda anabapeleka mumanja uya Yosefe, ndipo iye anabasamalila. Bana nkhala mu jele kwa kantawi. 5 Bonse babili bana lota chiloto, wopasa chakumwa na opanga bulendi ya mfumu ya ku Igupto pamene banali mu jele. Aliyense anali na chiloto usiku umozi, ndipo chiloto chili chonse chinali ndi chivumbuluso. 6 Yosefe anabwela kuseni mukubaona. Onani banali osakodwela. 7 Anafunsa bakulu bakulu ba Farso bamene banali naye mu jele mu nyumba ya bwana wawo, nati nanga nichani muoneka osakondwela lelo? 8 Iwo bana muyanka, bonse talota chiloto ndipo kulibe aliyense angamasulile. " Yosefe anabauza, " Kodi kumasulila sikwa Mulungu niuzeni, napapapta." 9 Mukulu opeleka chakumwa anamu uza chiloto chake Yosefe. Anamu uza kuti, onani, mutengo unali pasongolo panga. 10 Mumutengo munali ntambi zitatu. Pamene unapulika, maluba anachoka ndipo unabala mpesa zakupya. 11 Chiko cha Farao chinali mumanja mwanga. Ninatenga mpesa nakuzi fyantila mu chiko cha Farao, ndipo ninaika chiko mumanja mwa Farao." 12 Yosefe anati kwa iye, iyi ndiye tantauzo lake. Ntambi zitatu ni masiku atatu. 13 Mu masiku yatatu Farao azakuchosa mu jele nakukubweza pa chito yako uzaika chiko mumanja mwa Farao, monga mwamene unalili opeleka chakumwa. 14 Koma ukaniganizileko zikayenda bwino naiwe. Ukamu uze Farao pali ine kuti akani choseko muno mu jele. 15 Popeza ine ninali monga ogwiliwa kuchokela ku ziko la Ahebri, ngankhale kuno, sininalakwe kali konse kuti ni pezeke mu jele muno." 16 Pamene mukulu opanga bulendi anaona kuti kuvumbulusa kunali bwino, anati kwa Yosefe, " Naine nenze na chiloto ndipo, onani mabasiketi yatatu ya buledi yanali pa mutu panga. 17 Mu basiketi ya pamwamba munali zosiyana siyana za kudya za Farao, koma tunyomi tunadya mu basiketi inali pa mutu panga." 18 Yosefe ana yanka nati, " Iyi ndiyo tantauzo. Mabasiketi yatatu ni masiku atatu. 19 Mu masiku yatatu Farao azakuchosa mu jele ndipo azakupachika pa mutengo. Ndipo tunyoni tuzadya tupi yako. 20 Kunabwela kuti pasiku la chitatu, linali siku lakukumbukila kubadwa kwa Farao. Anapanga madyelelo yabanchito bake bonse. Kumwa na mukulu wopanga buledi, kuli ba nchito bake. 21 Ana mubweza panchito yake mukulu wopeleka chakumwa ndipo anaikanso chiko mumanja mwa Farao. 22 Koma anapachika mukulu wa opanga buledi, monga mwamene Yosefe anavumbulusila kwa iwo. 23 Koma mukulu wa opeleka chakumwa uja sanamukumbukile Yosefe, ndipo anamuibala.