Mutu 3

1 Lomba njoka yenze yocenjera maningi kucila vinyama vonse vamsanga vamene yawe Mulungu anapanga. Anakamba kuli muzimai, " Nanga Mulungu anakamba kuti, ' Musadye kumutengo uliwonse mu munda?" 2 Muzimai anauza njoka kuti, " Tingadye cipaso chamu mitenga ya munda, 3 koma pali mutengo wamene uli pakati pa munda, mulungu anakamba kuti, ' simungadye, kapena kucigwira, olo muzamwalira.'" 4 Njoka inakamba ku muzimai," Simuzamwalila. 5 Pakuti mulungu aziwa kuti tsiku muzakadya mesnso yako ya zakasenguka, ndiposo uzaka nkhala monga mulungu, kuziba voipa na vabwino. 6 " Pamene muzimai anaona kuti mtengo niwabwino kudya, ndipo nio kondweresa menso, ndipo mtengo wenze wopasa cilako lako copusa munthu nzelu, mukazi anatengapo cipaso anadya anadya ndipo anapasako mwamuna wake wamene enze na eve, ndipo anadya. 7 Menso yao wonse babili ya nasenguka, ndipo bana ziba kuti binali cinthuko. Anatenga matepo ya mutengo anampanga vovala vao. 8 Bana mvera mudidi ua Yehova Mulngu ayenda mu munda mumazulo, ndipo mwamuna na mukazi wake anazibisa beka kutoka ku menso ya Yehova mulungu mu mitengo zamu munda. 9 Yahova Mulungu anaitana mwamuna nakumufunsa kuti, " Uli kuti?" 10 Mwamuna anayankha kuti, " Nakumverari mu munda, nenze na mantha, ndaba nenze cinthako. Nenze nabisama." 11 Mulungu anakamba, " Nindani akuuza kuti wenze cinthako? Kodi wadya mumtengo nina kulesa kuti osadyamo?" 12 Mwamuna anakamba kuti, " Muzimai wamene munanipasa kunkhala naye, ananipasa cipaso camumtengo, ndipo ndinadya." 13 Yehova mulungu anakamba kuli mudzimai, " nivichani vamene wacita?" Muzimai anakamba kuti, " Njoka inani nama, ndipo ndinadya." 14 Yheva Mulungu anakamba na njoka, " Cifukwa wacita ici, iwe weka ndiwe wotembelereka pakati kavinyama vamsanga. uzayamba kuyenda na mala yako, ndipo ndi dothi uzadya masiku yonse ya moyo wako. 15 Ndizaipo kuzondana pali iwe na muzimai, na pakati ka mbeu yako na yake. Azamiyula mutu wako, ndipo iwe uza myula kadenene kake." 16 Kuli muzimai anakaba kuti, " Nizaika maningi kubabo mukubala bana kwako; ni muvobaba uzabala bana bako. Kufuna kwako kuzakuala kwamwamuna wako koma azakulamulila." 17 Kuli Adamu anakamba kuti, "Cifukwa wa mwera mau ya mkazi wako, wadya kucokela mumtengo, wamene ninaku uza kuti osadyemo,' yotembelereka ni nthaka cifukwa cha iwe; masik yonse uzadya kupitila munchito zobaba. 18 Izakulelela minga nazolasa ndipo uzadya vomera mumunda. 19 Na cibe capamenso yako uzadya mkate, pakana ubwerere ku dothi, ndaba ndiye kwamene unacoka. Iwe ndiwe dothi, na kudothi uzakabwerela." 20 Mwamuna anaitana mkazi wake Eva cifukwa enze mai wa vamoyo vonse. 21 Yehova Mulungu anapangira Adamu na mkazi wake vovala vavikumba nakubavalika. 22 Yehova Mulungu anakamba, Manje munthu ankhala monga ise kuziba voipa na vabwino. Manje safunika kuvomekezewa kufika kufupi, ndi kutenga mu mtengo wamoyo, nakudya, na kunkhala namoyo inthawi zonse." 23 Ndipo Jehova Mulungu ana mucosamo mu munda, wa Edeni kuti akalime mu nthaka mwamene ana coka. 24 Ndipo Mulungu anacosamo mwamuna mu munda, ndipo anaikapo kelebimu ku mawa kwa munda wa Edeni, na lupanga yoyaka yamene yenze kupidamuka kulikonse, cifukwa cosonga njira yoyenda ku mtengo wamoyo.