Mutu 24

1 Manje Abrahamu anali anakula maningi ndipo Yehova anamudalisa Abrahamu muvinthu vonse. 2 Abrahamu anati kwa wanchito wake, wamene anali mukulu pa nyumba yake ndiponso wamene anali kulamulila zonse anali nazo, "faka kwanja kwako pansi pa chibelo changa. 3 Ndipo nizakulapisa iwe pa Yehova, Mulungu wakumwamba, ndi Mulungu wapansi, kuti usakamutengele mukazi mwana wanga mwamuna kuchokela kwa Akenaniwo, mwamene napanga nyumba yanga. 4 Koma uzayenda ku Ziko yanga, kuli ba bale banga nakumutengela mukazi mwana wanga Isaki. 5 Wanchito anakamba naye kuti, nanga ngati mukazi sazafuna kunikonkha kuziko lino? Nizakamutenga mwana wanu ku Ziko kwamene munachokela imwe? 6 Abrahamu anamuuza kuti, "uone kuti usakamutenge mwana wanga kwamene uko. 7 Yehova Mulungu wakumwamba, wamene ananitenga ine kuchoka kunyumba ya batate banga na ku Ziko laba bale banga wamene anakamba na ine na kulumbila kwa ine kuti, ku mbeu zako nizakupasa iyi Ziko,''wamene azatuma mungelo kuyenda pasogolo pako kuti akusogolele kutenga mukazi wa mwana wanga kwamene uko. 8 Koma ngati mukazi sazafuna kukukonkha iwe, uzankhala omasuka pakulapila kwanga. koma siufunika kutenga mwana wanga kwamene uko. 9 Ndipo wanchito anaika kwanja kwake pansi pa chibelo cha Abrahamu bwana wake, ndipo analapila kwa iye pa chintu chamene icho. 10 Wanchito anatenga kuchokela kwa bwana wake ngamira zili teni ndipo anayambapo. Anatenganso mpaso zosiyana siyana kuchokela kuli ba bwana bake. Ananyamuka na kuyenda ku gawo la Aramu Naharaimu, ku muzinda wa Nahori. 11 Anagwadisa ngamira kunja kwa muzinda kuchisime cha manzi. Iyi inali ntawi yakumazulo pamene bakazi banachoka kuyenda mukutapa manzi. 12 Ndipo anati, "Yehova, mulungu wa ba bwana banga ba Abrahamu, nipaseni kupambana ine lelo ndi kukulupilika kwanu muchipangano ndi Bwana wanga Abrahamu. 13 Onani, Ine naimilila pa chisime cha manzi, ndipo nana bakazi ba mu muzinda babwela mu kutapa manzi. 14 Lekani chichitike motele, nikauza musikana, "napapata bweza pansi mugomo wako kuti nimweko manzi, ndipo azakamba kuti, Imwa, ndipo nizamwesanso na ngamira; wamene uyo ankhale mukazi osankila kapolo wanu Isaki. Pali ichi nizaziba kuti mwalangiza kukulupilika kwa chipangano kwa bwana wanga. 15 Chinachitika kuti pamene akalibe kusiliza kukamba, Onani, Rebeka anachoka ndi mugomo wake pa pewa. Rebeka anabadwa kwa Batuele mwana wa mwamuna wa Milika, mukazi wa Nahori, mubale wa Abrahamu. 16 Uyu mukazi anali wabwino ndiponso anali namwali. Sanazibepo mwamuna. Anaselukila ku chisime, ndipo anazulisa mugomo wake nakukwela pamwamba. 17 Ndipo wanchito anatamanga kuti akumane naye nakukamba kuti, napapata nipaseko yang'ono manzi mu mugomo wako. 18 Änati, Imwa, bwana wanga,"ndipo anayendesa nakubweza pansi mugomo wake mu manja mwake nakumupasa cha kumwa. 19 Pamene anasiliza kumupasa chakumwa, anati, "Nizatapa manzi ya ngamira zako, mpaka zimwe zonse." 20 Ndipo anayendesa na kuchosa mu mugomo nakufaka muchomwelamo, nakutamangila kuchisime mukutapa manzi ya ngamira zonse." 21 Mwamuna anamulangana iye osakamba kanthu kuona kuti kapena Yehova anamuyendesa bwino mu ulendo wake kapena iai. 22 Pamene ngamira zinasiliza kumwa , mwamuna anachosa mpete yapampuno ya golide kulemela kwake sikelo lateka, na vibili va golide vibango vaku manja kwake volemela teni lateka. 23 Ndipo anafunsa, "Ndiwe mwana wa bandani? Niuze napapata, kodi kuliko malo kuli ba tate bako kunyumba tigoneko usiku? 24 Anayankha kuti, Ine ndine mwana wa Betuele mwana wa wamwamuna wa Milika, wamene anabala kwa Nahori." 25 Anamuuza futi nati, tili na wambili uzu na vakudya ndiponso na malo yogonamo usiku. 26 Mwamuna anagwada na kuyamika Yehova. 27 Anati, adalisike Yehova Mulungu wa bwana wanga Abrahamu, wamene sanakane ku kulupilika kwa chipangano ndi chifundo chake mwa bwana wanga. Koma monga ine , Yehova anisogolela munjila ya kunyumba ya ba bale ba bwana wanga. 28 Ndipo mukazi wachichepele anatamanga nakuuza baku nyumba ya ba Mai bake vonse vintu. 29 Manje Rebeka anali na mulongsi wake zina lake Labani. Labani anatamangila mwamuna wamene anali kunja kumuseu waku chisime. 30 Pamene anaona mpete ya pampuno ndi vibango vakumanja kuli kalongosi wake, na pamene ananvela mau ya Rebeka mulongosi wake, ivi ndiye vamene mwamuna aniuza, anayenda kuli mwamuna, ndipo onani, anaimilila na ngamira pa chisime. 31 Ndipo Labani anati, "bwela, Iwe wodalisika wa Yehova. Ni chani uimilila panja? Nakonza nyumba na malo ya ngamira." 32 Ndipo mwamuna anabwela kunyumba nakumasula ngamira. Ngamira zinapasidwa mauzu na vakudya, na manzi yanapasidwa kuti asambe kumendo na mendo yaba muna bonse banali naye. 33 Banamukonzela vakudya, kuti adye, koma anati, sinizadya nikalibe kukamba vamene nifuna kukamba. "Koma Labani anamuuza kuti, "Kamba." 34 Anamuuza kuti, ndine wa nchito wa Abrahamu." 35 Yehova anamudalisa bwana wanga kwambili ndiponso niolemela. Anamupasa iye nkosa na ng'ombe, siliva na golide, ba nchito bamuna na bakazi, ndi ngamira naba bulu. 36 Sara, mukazi wa bwana wanga, anabala mwana mwamuna kwa bwana wanga pamene bwana wanga anakota, ndiponso anamupasa vonse vinali vake. 37 Bwana wanga ananilumbilisa ine kuti, usamutengele mwana wanga mukazi waku Kanani, mu malo mwamene ine ninkhala. 38 Koma, uyende ku banja ya batate banga, nakuli ba bale banga, nakutenga mukazi wa mwana wanga. 39 Nizamuuza bwana wanga, "nanga ngati mukazi sazanikonkha." 40 Koma ananiuza kuti, "Yehova wamene niyenda naye, azatuma mungelo na iwe nakukudalisa munjila yako, kuti umutengele mwana wanga kuchokela kuli ba bale banga na kuli ba banja ba batate. 41 Koma uzankhala omasuka ku chipangano changa ukabwela kuli ba bale banga iye kuli iwe. Ndipo uzankala omasuka ku chipangano changa. 42 Ndipo nafika lelo ku chisime cha manzi, nakukamba, Yehova, Mulungu wa bwana wanga Abrahamu, napapata, ngati muzaniyendesa bwino munjila yanga- 43 Nilipo pano, naimilila pa chisime cha manzi---lekani mukazi azabwela kutapa manzi, mukazi wamene nizauza, napapata nipaseko manzi yang'ono mu mugomo wako kuti nimwe." 44 Mukazi azaniuza ine, "Imwa, ndiponso nizapasa manzi na ngamira zako."lekani ankhale mukazi inu, Yehova, mwamusankha wa mwana wa bwana wanga! 45 Nikalibe kusiliza kukamba mumutima mwanga, Onani, Rebeka anachoka ndi mugomo wake pa pewa yake, na kuselukila ku chisime na kutapa manzi. Ndipo ninamuuza, napapata nipaseko manzi yakumwa. 46 Mwamusanga anatula mugomo wake pachipewa nati, "Imwa, ndiponso nizapasa ngamira zako manzi. Ndipo ninamwa, ndipo anamwesanso na ngamira. 47 Ninamufunsa nati, ndiwe mwana wa bandani? anati, ndine mwana wa Betuele, mwana wa mwamuna wa Nahori, wamene Milika anabala kwa Iye. Ndipo ninafaka mpete pampuno yake na vibango kumanja yake. 48 Ndipo ninagwesa nkope yanga na kulambila Yehova, na kutokoza yehova, nakudalisa Yehova, Mulungu wa bwana wanga Abrahamu, wamene ananisogolela ine munjila, kuti nikamupezele mwana mukazi wake wa banja ya bwana wanga wa mwana wake mwamuna. 49 Sopano, ngati muli okonzeka kulangiza chikondi cha zoona na chikulupililo kwa bwana wanga, niuzeni. Ngati iai, niuzeni, kuti nipatukile ku kwanja kwaku manja kapena kukwanja ya manzele. 50 Ndipo Labani ndi Batuele anayankha kuti, Ichi chintu chachokela kwa Yehova: Sitingakambe kwa iwe choipa kapena chabwino. 51 Onani, Rebeka ali pamenso pako, mutenge ndipo uyende, kuti ankhale mukazi wa mwana mwana wa bwana wako , mwamene Yehova akambila." 52 Pamene wanchito wa Abrahamu ananva mau yawo, anagwesa nkope pansi pamenso ya Yehova. 53 Wancito uyu anatulusa zabwino za siliva na zabwino za golide, na vovala nakumupasa Rebeka. anapasanso mpaso zabwino kwa mubale wake nakuli ba Mai bake. 54 Ndipo iye na bamuna anali nawo ba nadya na kumwa. Banankhala kuja usiku bonse, ndipo pamene banauka kuseni, anati, nitumeni kwa bwana wanga. 55 Mubale wake na ba Mai bake banati, lekani mukazi mun'gono ankhale naife masiku yang'ono masiku yali teni. 56 Koma anabauza kuti, "musanichingilize, chifukwa Yehova ananidalisa munjila yanga. Nitumeni kuti ningayende kuli bwana wanga. 57 Banati, "tizamuitana mukazi wamung'ono nakumufunsa." 58 Ndipo banamuitana Rebeka nakumufunsa, "uzayenda nauyu mwamuna?"Iye anayankha, "Nizayenda." 59 Ndipo banamutuma kalongosi wawo Rebeka, pamozi naba nchito bake bakazi, muulendo wake pamozi ndi wanchito wa Abrahamu na banthu bake. 60 Banamudalisa Rebeka nati, "mulongosi watu, leka unkhale make wa bana wanu sauzandi ndi teni sauzandi, ndipo leka bana bako batenge makomo ya bonse bamene babazonda. 61 Ndipo Rebeka ananyamuka, iye naba nchito bake bakazi nomanga pa ngamira, nakumukonkha mwamuna. Wanchito uja anamutenga Rebeka nakuyenda naye. 62 Isaki anali kunkhala ku Negev, ndipo anachokela ku Beer Lahai Roi. 63 Isaki anachoka kuyenda mukuganiza mu munda kumazuloNdipo analangana kusogolo nakuona, Onani, kunali ngamira zinali kubwela." Rebeka analangana, pamene anaona Isaki, anaseluka pa ngamira. 64 Anauza wanchito wake, "Nindani uja mwamuna wamene ayenda mumunda kubwela kuti akumane naife? 65 Wanchito anati, "Ni bwana wanga."Ndipo iye anachosa chovinikila kumenso, nakuzivinikila. 66 Wanchito anamuuza Isaki vonse vamene anachita. 67 Ndipo Isaki anamubwelesa iye kunyumba kwa Sara amai bake, nakumutenga Rebeka, nakunkhala mukazi wake, ndipo anamukonda. Ndipo Isaki anatontozedwa pambuyo pa infa ya ba Mai bake.