Mutu 9

1 David anakamaba kuti, "Kosi kuli aliyense osalila mu banja ya Sauli kuli enve kuti ni kamu onesele chifundo kamba ka Jonatani?" 2 Kunali mu banja ya Sauli wanchito wamene zina yake Zuba, anamuyitana kuli Davidi. Mfumu ina kamba kuli enve kuti, "Kodi ndiwe Ziba?" Anayanka "Indee. Ndine wanchito wanu." 3 Chakuti mfumu ina kamba kuti, "Kulibe anasala munyumba ya Sauli wamene ninga chitile chifundo cha Mulungu?" Ziba anayanka kuli mfumu, "Jonatani akali na mwana mwamuna, wamene olemala mumendo mwake." 4 Mfumu ina kamba kuli enve, "Alikuti?" Ziba anayanka kuli mfumu, "Onani, ali munyumba ya mwana wa Makiri wa Ammeli ku Lo Diba." 5 Pamene apo mfumu Davidi anamuitana kumu bwelesa kumu chosa mu nyumba ya mwana wa Ammieli ku chokela ku Lo Diba. 6 Manje Mefiboshiti mwana wa Jonatani mwana wa Sauli ana kwela kuli Davidi naku gwada nkope yaje pansi ku chitila Davidi ulemu. Davidi anakamaba uti, "Mefibosheti, "Anayanka, "Onani, Ndine wanchito wanu!" 7 Davidi ana kamba kuli enve kuti, "usayope, ndaba miku onesa chifundo chifukwa cha Jonatani tate wako, ndipo niza bwezela kuli iwe malo yonse ya Sauli bambuye bako, azayamba kudia ntawi zonse pa tebulo yanga." 8 Mefibosheti anagwada naku kamba kuti, "Nindani wanchito wanu, wamene mu onesela chisomo pali galu ya kufa monga ine?" 9 Pamene apio mfumu inaitana Ziba, wanchito wa Sauli, nak kamba kuli enve, "vonse vinali va Sauli na banja yake na vipasa kuli muzukulu wa bwana wako. 10 Iwe, na bana bako, ndipo ba nchito bako bafunikila kumulimila munda wake ndipo mufunikila kukolola vakudya mwakuti muzukulu wa bwana wako akankale na vokudya. kuli Mefibosheti, Muzukulu wa bwana wako afunikila ntawi zonse kudya pa tebulo yanga." Manje ziba anali na bana bamuna kumi naba sanu naba chito ma kumi yabili. 11 Pamene apo Ziba anakamba kuli mfumu, "Wanchtio wanu azachita vonse bwana wanga mwamene mwalamulila wanchinto wanu. "Mfumu ina onjezelapo, "Monga kuli Mefibosheti azadya pa tebulo yanga, monga umozi wabana bafumu banga." 12 Mefibosheti nali na mwana wamene zina yake anali Mika. Bonse bamene benze kunkala mu nyumba ya Ziba benze banchito ba Mefibosheti. Manje 13 Mefibosheti anankala mu Yelusalemu, ndipo anali kudya pa tebulo ya mfumu, inga nkale enze olemala mendo yonse.