Mutu 9

1 Yesu anangena mu bwato, naku enda kumbali kwina kwa nyanja, nakufika ku muzinda kwake. 2 Onani, banamuletela muntu wama manjenje aligone pa mpasa. Pamene anaona chikulupililo chabo, Yesu anamu uza uja muntu, "Mwana, nkala okondwela. Machimo yako yakululukiwa." 3 Onani, benangu pali bolemba banayamba kukamba pabeka kuti, "Uyu muntu anyoza." 4 Yesu anaziba maganizo yabo naku bauza kuti, "Nanga nichani imwe muganiza voipa mumitima zanu? 5 Nanga nichiti chintu chamene sichishupa, kukamba kuti, 'Machimo yako yakululukiwa,' kapena kukamba kuti, 'Ima uyende'? 6 Koma kuti imwe muzibe kuti Mwana wa Muntu alinayo mpavu pa ziko yo kululukila machimo, ... anakamba ku uza uja wamanjenje kuti, "Imilila, tenga mpasa yako, enda kunyumba kwako." 7 Pamene apo mwamuna uja ananyamuka naku enda kunyumba kwake. 8 Pamene gulu ya bangtu inaona ivi, banadabwa nakuyamba kutamanda Mulungu, wamene anapasa mpavu zamutundu uyu ku bantu. 9 Pamene Yesu anali kupita paja, anaona muntu zina yake Mateyo ali nkale posebenzela baja bamusonko. Anamu uza eve kuti, "Nikonke." Anaima nakumukonka. 10 Pamene Yesu anankala kuti adye munyumba, onani, bambili ba musonko na bamachimo banabwela nakudya pamozi na Yesu na bopunzila bake. 11 Pamene ba Falisi banaona ivi, banakamba kuli bopunzila ba Yesu kuti, "Nanga kansi nichani chamene bapunzinsi banu badyela pamozi naba musonko na bantu bama chimo? 12 Pamene Yesu anamvel aivi, anakamba kuti, "Bantu bamene bali bwino mu mubili sibafunika kuona dotolo, koma baja bamene nibodwala. 13 Endani muka punzile tantauzo ya kukamba uku: 'Ine nifunapo kunkala na chifundo kuchilapo nsembe.' Chifukwa ine sininabwele kuitana bolungama kuti batembenuke, koma bamachimo. 14 Bopunzila ba Yohane banabwela kuli eve nakukamba kuti, "Nanga nichani ise na ba Falisi timazi mana chakudya kambili, koma bopunzila banu beve sibama zimana?" 15 Yesu anaba yanka, "Nanga bantu boitaniwa ku ukwati banga mvese chifundo pamene okwatiliwa akali nabo? Koma ma siku yazakabwela pamene okwatiliwa azakatengewa, pamene apo bazakazimana chakudya. 16 Kulibe muntu wamene aika kanyula ka manje pali chovala chakudala, chifukwa kanyul aaka kazangámba chovala, kungámbika kweve kuzankala kukulu. 17 Nafuti bantu sibamaika vinyo va manje mu voikamo vakudala. Ngati bachita ichi, voikamo vizapwanyika, vinyu vizataika, na voikamo vizaonongeka. Koma, bamaika vinyu va manje mu voikamo vamanje, munjila iyi vonse visasungiwa chabe bwino. 18 Pamene Yesu anali kubauza ivi vintu, onani, kazembe umozi anabwela naku gwada kuli Yesu. Nakukamba kuti, "Mwana wanga mukazi amwalila, koma bwelani mumuike kwanja, azauka." 19 Pamene apo Yesu anaima naku mukonka, na bopunzila bake na beve banakonka. 20 Onani, mukazi wamene anali na vuto yochoka magazi zaka zopitilila kumi ya zibili anabwela kumbuyo kwa Yesu naku gwila kunyansi ya chovala chake. 21 Chifukwa anaziuza mukazi uyu eka kuti, "Ngati chabe nagwila vovala vake, Ine nizankala chabe bwino." 22 Koma Yesu anapindimuka naku muona, nakukamba kuti, "Mwana wanga mukazi, nkala olimba, kukulupilila kwako kwaku polesa." Pamene apo uja mukazi anapola. 23 Pamene Yesu anafika munyumba ya uja kazembe, anaona bolinza mitoli na gulu ya bantu ipanga chongo. 24 Anabauza kuti, "Tiyeni endani, uyu mukazi sanamwalile, koma agona chabe." Koma banamu seka monyezela. 25 Pamene gulu ija inachoka panja, anangena mu chipinda naku mugwila kukwanja, mukazi uja anauka. 26 Nkani ya uyu utenga ina enda mumalo yonse. 27 Pamene Yesu anali kupita kuchokela kuja, bamuna babili bamen banalibe menso banamukonka. Banapitiliza kupunda naku kamba kuti, "Tichitileni chifundo ise, Mwana wa Davide!" 28 Pamene Yesu ananegna munyumba, bamuna baja banalibe menso banabwela kuli eve. Yesu anabauza kuti, "Mukulupilila kuti ninga kwanise ichi?" Bana muyanka kuti, "Inde, Ambuye." 29 Pamene apo Yesu anabagwila pamenso nakukamba kuti, "Lekani chikuchitikileni kulingana na chikulupililo chanu," 30 na menso yabo yanaona. Yesu anabauza mobalimbikisa kuti, "Onani kuti kulibe muntu ali onse wamene azaziba ichi." 31 Koma bamina baja babili bana enda naku peleka mau ku malo yonse yakuja. 32 Pamene baja bamuna banali kuenda, onani, mwamuna chiulu wamene anali na vibanda banamuleta kuli Yesu. 33 Pamene chibanda chinachosewa, uja chibulu anayamba kukamba. Ma gulu ya bantu yana dabwa nakukamba kuti, "Ichi chikalibe kuonekapo mu Islayeli!" 34 Koma ba Falisi beve banali kukamba kuti, "Nichifukwa cha mukulu wa vibanda, ndiye chamene akwanilisila kuchosa vibanda." 35 Yesu anaenda-enda mumizinda na muminzi yonse. Anapitiliza kupunzisa muma sinagogo yabo, kulalika utenga wa ufumu na kupolesa matenda yamu tundu onse na kusamvela bwino kosiyana-siyana. 36 Pamene anaona magulu, anamvela chifundo, chifukwa banali bovutika mitima nafuti bobwezewa kumbuyo. Banali monga nkosa zamene zilibe ozibeta. 37 Anakamba kuli bopunzila bake kuti, "Vokolola nivambili, koma banchito ndiye bamene bachepa. 38 Chifukwa chake imwe muyenela kupempela kuli Ambuye ba vokolola, kuti batume banchito mu munda wabo."