Mutu 8

1 Pamene Yesu anaseluka ku pili, magulu ya bantu yanamukonka. 2 Onani, muntu wa makate anamukonka na kugwada pansi, nakukamba kuti, " Ambuye, ngati mufuna, mungani polese." 3 Yesu anatambasula kwanja yake naku mugwila, naku kamba kuti, " Nifuna. Pola." Pamene apo eve anapolesewa ku matenda yake ya makate. 4 Yesu anamuuza kuti, " Onesesa kuti usauze muntu aliwonse kantu. Yenda, kazilangize kuli mukulu wa nsembe, na kupeleka chopeleka chamene Mose anakuuzani, kupeleka umboni kuli beve." 5 Pamene anali kubwela ku Kapenamu, mukulu wabasilikali anabwela kuli eve, kumupempa 6 nakukamba kuti, "Ambuye, wantchito wanga kunyumba aligone adwala alibe mpavu ndipo amvela kubaba kukulu." 7 Pamene apo Yesu anamuuza kuti, " Nizabwela nimupolese." 8 Eve mukulu wa asilikali anamuyanka nakuti, "Ambuye, ine sindine oyenela kuti imwe mubwele kungenda munyumba yanga. Koma kambani chabe mau wantchito wang aazapola. 9 Chifukwa ine ndine muntu wamene ali pansi pa bakulu bantchito, naine nilinabo basilikali pansi panga. Nikamuuza umozi kuti, 'yenda,' amayenda, nakuli winangu kuti, 'bwela,' amabwela, nakuli wantchito wanga kuti, 'Chita ichi,' amachita." 10 Pamene Yesu anamvela ivi, anadabwa nakuuza bantu bamene banali kumukonka kuti, "Zoona nikuuzani imwe, nikalibe kupezapo muntu aliwonse wamene ali na chikulupililo monga ichi mu Israeli. 11 Nikuuzani kuti, bantu bambili bazakabwela kuchokela kumawa na ku mazulo, ndipo bazankala pamalo podyela pamozi na Abrahamu, Isaki, na Yakobo, mu ufumu wakumwamba. 12 Koma bana ba mu ufumu bazataiwa panja mumu mudima, kwamene kuzankala kulila na kusheta meno." 13 Yesu anakamba kuli uja mukulu waba silikali, "Yenda! Monga mwamene wakulupilila, leka chikuchitikile iwe." Uja wantchito wake anapolesewa pa ntawi yamene ija. 14 Pamene Yesu anabwela munyumba ya Petulo, anaona bapongozi ba Petulo baligone namatenda ya kupya tupi. 15 Yesu anagwila kwanja yabo, kupya tupi kunayenda pamene apo. Banaima na nakuyamba kumusebenzela. 16 Pamene kunankala ntawi yaku mazulo, bantu banaleta kuli Yesu bantu bambili bamene banali na zibanda. Anabachosa vibanda kusebenzesa chabe mau nakupolesa bonse bamene banali namatenda. 17 Munjila iyi mau yamene yanakambiwa na muneneli Yesaya yanafikilisiwa, kukamba kuti, "Eve eka anatitengela kusamvela bwino kwatu naku nyamula matenda yatu." 18 Manje pamene Yesu anaona gulu yabantu banamuzungulukila anabauza kuti bachokeko bayenda kumbali ina ya Galili. 19 Ndipo eve wolemba anabwela kuli Yesu nakukamba kuti, "Mupunzisi, ine nizakukonkani kuli konse kwamene imwe muzayenda." 20 Yesu anamuuza kuti, "Nkandwe zili na monkala, tunyoni twa mumwamba tuli nato tuchisa, koma Mwana wa muntu eve alibe na poika mutu." 21 Wina pali wopunzila anamuyanka kuti, "Ambuye, nivomeleseni kuti niyende nikashike ba tate banga." 22 Koma Yesu anamuuza kuti, "Konka ine, baleke bakufa bashikane beka." 23 Pamene Yesu anangena mu bwato, bopunzila bake banamukonka. 24 Onani, kunabwela chimpepo chikulu pa nyanja, mwakuti bwato inazula na manzi. Koma Yesu anali akali gone. 25 Bopunzila bake banenda kuli eve na kumuusha, nakumuuza kuti, "Tipulumuseni, Ambuye; tifuna kufa! 26 Yesu anakamba kuli beve kuti, "Nanga nichani muli na manta, imwe bochepa chikulupililo?" Anaima naku kalipila chipempo na nyanja. Chipempo chinabwela chasila. 27 Bantu baja banadabwa kwambili nakukamba kuti, "Nanga nimuntu wa bwanji kansi uyu, wamene na chimpepo na nyanja vimumvelela?" 28 Pamene Yesu anabwela kumalo kwina ku ziko yaku ba Gadalene, bamuna babili bamene banali na vibanda banamukumanya eve. Banali kuchokela ku manda ndipo banali ba ndeo, chifukwa chake kulibe muntu wamene anali pa ulendo wamene anali kupitila njila iyi. 29 Onani, banapunda nakukamba kuti, "Nanga nichani chamene ufuna kuli ise iwe, Mwana wa Mulungu? Nanga wabwela kuno kuti utizunzise pamene ntawi yamene inaikiwa ikalibe kufika?" 30 Manje gulu ya nkumba inali kudya, osati kutali maningi na beve. Vibanda vinapitiliza kumupempa Yesu kuti, 31 "Ngati mwatichosa, tiuzeni tiyenda muli gulu ya nkumba." 32 Yesu anaviuuza kuti, "yendani!" Vibanda vinachoka nakuyenda mu nkumba; ndipo onani, gulu yonse ya nkumba zinataba nakuyenda kuseluka chulu kuyenda mu nyanja mwamene zinafela mumanzi. 33 Baja bamene banali ku betela nkumba banataba naku enda mu muzinda naku uza bantu vonse vamene vinachitika, maka-maka vamene vinachitika kuli baja bamene banali na vibanda. 34 Onani, muzinda onse unabwela kuti uone Yesu. Pamene banamu ona Yesu, banamupapatila kumupempa kuti achoke ku malo yabo.