Mutu 22

1 Yesu ananena kwaiwo kachibili mumyambi, ndikunena, 2 ''Ufumu wakumwamba uli monga mfumu inakonzekela pwando yachikwati wa mwana wake mwamuna. 3 Anatuma banchinto bake kuitana bonse bamene banaitaniwa kupwando yachikwati ichi, komanso sibanabwele. 4 Nafuti mfumu inaitana banchito bake, nakuti, ' Uzani baja woitaniwa, '' Onani, nakonzeka mugonelo wanga. Ng'ombe yanga natubana twake toina vapaiwa, ndiponso izi zonse nizokonzewa. Bwelani kupwando yaukwati.'' 5 Koma sianafakileko nzelu ndiponso anayenda, alibonse kuulimi wake, ndiponso wina kumalonda yake. 6 Benangu banagwila banchito bamfumu, ndiponso anamvesewa nsoni, nakubapaya. 7 Mfumu inakalipa na kutuma basilikali bake, ndiponso banapaya baja bopaya na kushoka muzinda yawo. 8 Ndipo anauza banchito bake kuti, 'Chikwati nichokonzekela, koma baja bamene banaitaniwa sibanali oyenela. 9 Mwaichi yendani pokumanilana njila ndi kuitana banthu bambili bamene mungakwanise kuitana kupwando yachikwati monga mwamene mungapezele.' 10 Banchito banayenda munjila, na kusonkanisa banthu pamozi bonse bamene banapeza, woipa na babwino. Na mumalo yokwatililamo chikwati yanazula na balendo. 11 Koma pamene mfumu inabwela mukati kuona balendo, Inaona mwamuna wamene sanavale zovala vaukwati. 12 Mfumu inamuuza kuti, ' Munzanga, wabwela bwanji kuno ulibe vovala vaukwati?' Koma uja mwamuna analibe mau. 13 Koma mfumu inauza banchito kuti, ' Mumangeni mwamuna uyu kumanja na mendo, ndipo mumutaile panja pofipa, pamene pazankhala kulila nakusheta meno.' 14 Koma banthu bambili nioitaniwa, koma wosankhidwa nibang'ono.'' 15 Ndipo bafalisi banayenda na kukonzekela mwamene bangamugwilile Yesu mumakambidwe yake. 16 Ndipo banatuma kuli eve bophunzila bake, pamozi nama Herodiya. Banamuuza Yesu kuti, '' Muphunzisi, tiziba kuti ndiwe wazoona, na kupunzisa njila za Mulungu. Siumasamalila maganizo ya aliyense, ndipo siulangiza kusanka pa banthu. 17 Koma tiuze, uganizapo bwanji? kodi nichovomelezewa kupasa musonko kuli kaisala kapena iyai?'' 18 Koma Yesu anaziba kuipa kwawo na kukamba kuti, '' Nichifukwa chani chamene muniyesela, imwe bachinyengo? 19 Nilangizeni ndalama zamisonko.'' Ndipo banabwelesa kobili kuli eve. 20 Yesu anakamba kuli beve, '' Nanga vili muchifanizilo na zina yabandani ivi? '' 21 Yesu anabauza kuti, '' kaisala.'' Ndipo Yesu anabauza kuti, '' Kansi pasani kuli kaisa zinthu zamene zili za kaisala, ndipo kuli Mulungu zamene zili za Mulungu.'' 22 Pamene banamvela ivi, banadabwisiwa. koma anamusiya ndikuchokapo ndipo banayenda 23 Pali ija siku masadusi benangu, bananena kuti kulibe chisinsimuso, anabwela kuli iye. Anamufunsa iye, 24 Nakunena, '' Aphunzisi, Mose ananena, ' ngati munthu afa, kopanda mwana, mubale wake afunika kukwatila mukaziwake na kumubalilako mubale wake. 25 Kunali babale bali 7. Oyamba anakwatila na kumwalila. Kosasiyapo mwana aliyense, Anasiya mukazi wake kuli mubale wake. 26 Ndipo mubale wake anachita chimodzimodzi, koma wachitatu, nakufikila kufikila naku mubale wa namba 7. 27 Kuchokela kwa aba onse, mukazi anafa. 28 Manje pakuukisiwa azankhala mukazi wandani pali aba babale bali 7? chifukwa onse anamukwatilapo mukazi uyu.'' 29 Koma Yesu anayanka ndiponso ananena kwaiwo, ''Ndimwe osoba, Chifukwa simuziba malemba olo mphamvu za Mulungu. 30 Koma pachisinsimuso sibamakwatila olo kupasiwa kuchikwati. Koma, ankhala monga angelo kumwamba. 31 Koma kulinganiza nazakuukisidwa kwa akufa, simunabelenge zamene zinanenewa kwainu ndi Mulungu, nakunena, 32 ' Kuti ndine Mulungu wa Abulahamu, ndiponso Mulungu wa Isaki, ndiponso Mulungu wa Yakobu'? Mulungu si Mulungu wa akufa, '' Koma ni Mulungu wa amoyo.'' 33 Pamene magulu inamvela izi, anadabwisiwa ndi kapunzhisidwe kake. 34 Koma pamene afalisi anamvela kuti Yesu abazizilika asadusi, anazikumaniza pamodzi iwo oka. 35 Wina waiwo, okambilako, anamufunsa funso, nakumuyesa_ 36 '' Aphunzisi, ni liti lamulo lalikulu pamalamulo?'' 37 Yesu ananena kwaiwo, '' Konda Mulungu wako namutima wako onse, namoyo wako onse, ndiponso ndi nzelu zako zonse.'' 38 Iyi ndiye lamulo ikulu yoyamba. 39 Ndiponso lamulo lacibili lili kuti_ ' Konda ozungulila iwe monga mwamene uzikondela.' 40 Pali aya malamulo yabili ndiye pamene yonse malamulo ndiponso aneneli ziimilila.'' 41 Koma pamene afalisi analipamodzi, Yesu anafunsa funso. 42 Ananena kuti, '' uganiza chani pali za khristu? Kodi ni mwana wandani?'' Ananena kwa iye, '' Ni mwana wa Davidi.'' 43 Yesu ananena kwaiwo, '' Chilibwanji, pamene Davidi alimumuzimu pamene amuitana Ambuye, nakunena, 44 Ambuye ananena kuli Mulungu wanga, '' Nkhala kuzanja lamanja, kufikila napanthawi yamene nizapanga adani ako kunkala pamapazi yako.'' 45 Ngati David amaitana kristhu 'Kuti Ambuye,' Angankhale bwanji mwana wa Davidi? 46 Kulibe wamene enze kukwanisa kumuyankha liwu ndiponso kulibe Munthu anayesa kumufunsa mafunso nafuti kuchokela siku ija.