Mutu 14

1 Pantawi ija, Helodi umozi mwa basogoleli anamvela uthenga wa Yesu. 2 Anauza bantchito bake kuti, "Uyu niwamene Yogane Obatiza; auka kubakufa. Ndiye chamene chilengesa mpavu kusebenza muli eve." 3 Chifukwa Helodi anamugwila Yohane, nakumumanga, nakumuika mu ndende chifukwa cha Helodiyasi, mukazi wa Filipu mubale wake. Chifukwa 4 Yohane anamuuza kuti, "Sichintu chovomelesewa kuti uyu ankale mukazi wako." 5 Helodi anafuna kumupaya, koma anali kuyopa bantu, chifukwa banali kumuyopa kukamba kuti nimuneneli. 6 Koma siku yokumbukila kubadwa kwa Helodi inafika, mwana mukazi wa Helodiyasi anavina pakati pa bantu nakumvesa bwino Helodi. 7 Pakuona ichi, anamulonjeza lonjezo molapa kuti azamupasa chintu chili chonse chamene azapempa. 8 Pamene bamai bake banamuuza vopempa, anakamba kuti, "Nipaseni apa manje, pa mbale, mutu mwa Yohani Obatiza." 9 Mfumu inakalipa maningi chifukwa cha chamene anapempa, manje chifukwa chakuti analapa na chifukwa cha baja bantu bamene banali naye pa chakudya chaku mazulo, anakamba kuti ichi chamene chichitike. 10 Anatumiza kuti bayende bamupaye Yohane mu ndende. 11 Ndipo mutu wake unabwelesewa pa mbale naku pasiwa kuli mwana mukazi uja wamene anautenga naku upeleka kuli bamai bake. 12 Bopunzila bake banabwela, nakunyamula thupi yake, naku yenda kuiika mumanda. Kuchoka apa, banayenda kukamuuza Yesu. 13 Manje pamene Yesu anamvela ichi, anachokako uku naku enda ku malo kwa eka. Pamene magulu yanamvela ichi, banamukonnka Yesu na mendo kuchokela mu mizinda. 14 Yesu anabwela kwamene kunali beve nakuona gulu ikulu maningi. Anamvela chifundo nakubapolesela bantu bodwala babo. 15 Ntawi yaku mazulo, bopunzila banabwela kuli eve nakumuuza kuti, "Kuno kumalo kulibe bantu, na ntawi yasila. Balekeni bantu, basiyeni bayende mu minzi kuti bakagule vakudya badye." 16 Koma Yesu anabayanka kuti, "Aba sibafunika kuti baende iyayi. Imwe mubapase vakudya." 17 Koma banamuyanka kuti, "Onani tili chabe na buledi ili 5 na nsomba zibili." 18 Yesu anayanka kuti, "Letani kuli ine." 19 Yesu anauza gulu kuti inkale pansi pa mauzu. Anatenga ma buledi yaja na nsomba zibili. Analangana kumwamba, anayadalisa ma buledi nakuya suna naku pasa bopinzila bake, na bopunzila bake banapasa ija gulu ya bantu. 20 Bonse banadya naku kuta. Banatenga vamene vinasalapo - votengelamo vili kumi na vibili. 21 Baja bamene banadya banali 5000 bamuna, kochoselako bakazi na bana. 22 Pamene apo anauza bopunzila bake kuti bangene mu bwato bayende kumbali kwina kwa nyanja, pamene eve anali kupisha bantu. 23 Pamene anasiliza kupisha bantu, anayenda pa chulu eka nakupempela. Pamene usiku unabwela, analipo eve eka. 24 Koma bwato inali kutali pakati pa manzi, inali kugwedezeka na chimpepo, chifukwa chimpepo chinali chikulu. 25 Mbanda kucha Yesu anafika kufupi na beve, nishi ayenda pa manzi. 26 Pamene bopunzila bake banamuona ayenda pa manzi, banavutika mutima nakukamba kuti, "Nichibanda," banalila na manta. 27 Koma Yesu anabauza pamene apo kuti, "Nkalani bolimba! Ndine! Osayopa iyayi." 28 Petulo anamuyanka nakukamba kuti, "Ambuye, ngati ndimwe, niuzeni kuti ine nibwele pa manzi." 29 Yesu anakamba kuti, "Bwela." Pamene apo Petulo anachoka mu bwato naku yenda pa manzi kuyenda kuli Yesu. 30 Koma pamene Petulo anaona chimpepo, anayopa, pamene anayamba kumbila, analila nakukamba kuti, "Ambuye, nipulumuseni! 31 Yesu pamene apo anatambasula kwanja yake, nakumugwila Petulo, nakumuuza kuti, "Iwe wachikululupilo chingóno, nanga nichani chamene wenze wakaikilila?" 32 Manje pamene Yesu na Petulo banangena mu bwato, chimpepo chija chinaleka. 33 Baja bopunzila bake bamane banali mu bwato banamupembeza Yesu naku kamba kuti, "Zoona ndimwe Mwana wa Mulungu." 34 Pamene beve banafika kumbali kwinangu kwa nyanja ija, banafikila kumalo yaku Genezaleti. 35 Pamene bantu bakuja kumalo banamuziba Yesu, bana tuma mau monse mu malo ya mumbali, ndipo banaleta bantu bonse bodwala. 36 Banamupapatila kuti bagwileko chabe chovala chake, ndipo bonse bamene banamugwila banapolesewa.