Mutu 1

1 Icho camene cenzeko kufumila pachiyambi, camene tinamvwa, camene tinaona na menso yatu, chamene tinapenyesesa, camene tinagwila ndi manja yathu - ichi ndiye ca Mau ya moyo. 2 Moyo, unazibisidwa, ndipo tauona, ndipo tiucitila umboni. Tikulalikilani kwa inu za umoyo wosatha, wamene unali ndi Atate, ndipo waziwika kwa ife. 3 Chija camene tinaona ndi kumva ticilankhulanso kwa inu, kuti munkhalenso ndi chiyanjano ndi ife. Chiyanjano cathu cili ndi Atate ndi Mwana, Yesu Kristu. 4 Futi tilemba vinthu ivi kuli imwe kuti chimwemwe cathu cinkhale cokwanila. 5 Uyu ndiye uthenga wamene tinamva, kucokela kwa iye ndi kulalikidwa kwa inu: Mulungu ndiye kuunika, ndipo mwayeve mulibiletu mudima. 6 Ngati tikamba kuti tili mucigwilizano ndi iye ndipo tuyenda mumudima, tikamba bodza ndipo siticita choonadi. 7 Koma ngati tiyenda mukuunika mwamene iye ali kuunika, ndipo mulopa wa Yesu Mwana wake utisukha kumachimo athu. 8 Ngati tinena kuti tilibe uchimo, tizinama ife toka, ndipo coonadi sicili mwa ife. 9 Koma pamene tivomeleza macimo athu, ali wokhulupilika ndi wolungama kutikhululukila machimo athu ndi kutisambisa ku chosalungama ciliconse. 10 Ngati tikamba kuti tilibe ucimo, tikumutenga iye kunkhala wa bodza, ndipo mau ake sali muli ife.