Mutu 5

1 Nabwela mu munda mwanga, mulongo wanga, muwatibwi wanga; Nasonkanisa mule wanga na zo nunkilisa zanga. Nadya chisa changa cha uchi na uchi wanga. Namwa vinyu wanga pamozi na mukaka wanga. 2 Ninali mutulo, koma mutima wanga unali menso. Pali phokoso ya wokondewa wanga agogoda naku kamba kuti, "Nisegulire, mlongo wanga, okondewa wanga, nkhunda yanga, wanga osadesewa, pakuti mutu wanga wanyowa na mame, stsi yanga ni chinyontho cha usiku." 3 "Navula mukanjo wanga; niyenela futi kuuvala? Nasuka mendo yanga; kodi niyafipise?" 4 Okondewa wanga ana genesa kwanja kwake pa nyumba ya chiseko, ndipo mutima wanga una khudziwa chifukwa cha eve. 5 Nina uka kuti nimusegulile okondewa wanga; manja yanga yanali kuchosa mule, tokumo twanga na mule wonyowa, chosegulila chiseko. 6 Nina segula chiseko cha okondewa wanga, koma okondewa wanga ana pidamuka naku yenda. Mutima wanga unagwa pamene anakamba. Nina mufunafuna, koma sinina mupeza; Nina muitana, koma sanani yanke. 7 Olonda ananipeza pamene anali kuzungulukila muzinda. Banani menya nakuni panga vilonda; olonda pamakoma anani poka chovala changa. 8 Nifuna ulumbile, bana bakazi baku Yelusalemu, kuti, mukapeza okodewa wanga- muzamuzibisa chani? - Nidwala chifukwa cha chikondi. 9 Nanga bwenzi wako apitililapo mwamuna wina okondewa, iwe okongola kwambili pali bakazi bonse? Chifukwa chani okondewa wako apitilila bokondewa benangu, kuti ufunse ise kutenga lumbilo yaso? 10 Okondewa wanga ni owala na maonekedwe yabwino, opambana pakati pa zikwi khumi. 11 Mutu wake ni golide woyengeka bwino; sisi yake ni yopobana koma yakuda ngati kwangwala. 12 Menso yake yali monga kunda pambali pa misinje ya manzi; osambisiwa na mukaka, okwela ngati miyala yamu tengo wapatali. 13 Mbovu zake zili ngati pogona pa zo nunkila, zo nunkira bwino. Milomo yake ili ngati maluwa, yochosa mule. 14 Manja yake yali na golidi yozunguliwa na myala yamu tengo yapatali. Mimba yake ni nyanga ya njovu yochigiliza na myala ya safiro. 15 Mendo yake ili kwati sadamila ya mwala obekelela, zoikwa pazisulo zagolide obekelela; Maonekedwe yake yali monga Lebanoni, yabwino kwati mikungudza. 16 Pakamwa pake ni po nzuna kwambili; ni okondeka mofikapo. Uyu ndiye okondewa wanga, ndiye muzanga wanga, Bana bakazi baku Yelusalemu.