Mutu 3

1 Usiku nili pa bedi yanga nenze kulakalaka wamene moyo wanga ukonda; Nina mfunafuna, koma sinina mupeze. 2 Nina zikambisa neka, "Niza uka naku kupyola pakati pa mzinda, kupyolela mu misewu na muma bwalo; niza fufuza wamene moyo wanga umkonda." Nina mfunafuna koma sinina mupeze. 3 Malonda ananipeza pamene anali kuzungulila mizinda. Nina funsa kuti, "Kodi mwaonako wamene moyo wanga nikonda?" 4 Panapita ka ntawi pang'ono nisanampitilile kwakuti nina mupeza wamene moyo wanga uma mukonda. Ninamu gwililila ndipo sinimu lekelako kuyenda kufikila ninamuleta 'munyumba yaba amayi banga, mu chipinda chogona cha amene ananipatsa bananibala. 5 Nifuna iwe ulumbile, mwana mukazi wa ku Yerusalemu, ndi mphoyo ndi nswala zamusanga, kwakuti siuzaka kapena kuusha chikondi kufikira akakondwera. 6 6Ni ciyani cilikubwela kucokela kucipululu kwati chusi, ozola kwati mule, na lubani, na unga watuntu wogulisiwa na bama londa? 7 Onani, ni pa bedi ya Solomo; Ankhondo makumi asanu nai modzi azunguluka, Amuna ba mpamvu bamu Israeli. 8 Bonse ni bakaswili na lupanga ndipo ni boziba nkondo. Muntu aliyense ali na lupanga yake mumusana mwake, okonzekela na zoyofiya za usiku. 9 Mfumu Solomo anzipangila yeka mu pando wamatabwa yochokera ku Lebanoni. 10 Nsanamila zake zinali za siliva; kubuyo kwake kwenze kwagolide, na mpando wa nyula zofiilila. Mukati mwake muna kongolesewa na chikondi na bana bakazi ba ku Yerusalemu. 11 Yedani bana bakazi baku Ziyoni, ndipo yang'anani Mfumu Solomo, letani chisote chachifumu ca mene amai bake bana muvalika pa siku yacikwati chake, pa siku ija. ya chisangalalo cha mutima wake.