Chapita 8

1 Yehova anakamba kwa Israyeli.'' Osayopa; osabwelela mumbuyo. Tenga bantu bonse bankhondo. Yenda ku Ai, nakupasa mumanja mwako mfumu ya ku ai, bantu bake, muzinda wake, na malo yake. 2 Vzacita kuli A na mfumu zake monga mwamene unacitila ku Yeliko na mafumu yake, koma votengwa na vobeta uzatenga. Vyike bantu kumbuyo kwa muzindi.'' 3 Ndipo Yoswa ananyamuka nakutenga bamuna bonse ku Ai, pamene apo Yoswa anasankha bamuna bali feti sauzande - okosa, bamuna ba mphavu - anabatuma kuyenda busiku. 4 Anabalamulila, ''onani, muzagonela kumbuyo kwa muzinda, osayenda kutali kucoka mu muzinda, koma monse imwe konzekani. 5 Ine nabamuna bonse bali naine tizafika ku mzinda, pamene ibo bakacoka ku menya ise, tizathaba kuli beve mongo tinacitila poyamba. 6 Bazacoka kutikonka paka tibacose ku muzinda. Bazakamba kuti, bali kuti thaba monga mwamene banathambila! naise tizabathaba. 7 Pamenepo muzacoka malo mwamene munabisama, nakulowa mumzinda. Yehova mulungu wanu azakupasani mumanja yanu. 8 Pamene mwagwila muzinda, muza ushoka, muzacita ivi pamene mwamvelela cilamulo capasiwa mumav ya Yehova ona, nakulamulila.'' 9 Yoswa anabatuma, banapita kumalo yabiamamo, na kubisama pakati ka Beteli na Ai ku mazulo ya Ai. koma usiku uja Yoswa anagona pakati ka banthu. 10 Yoswa anabuka kuseni maningi na ku konzekela basilikali bake, Yoswa na bakulu ba Israyeli, na kumenya bathu baku Ai. 11 Bamuna bonse bankhonda bamene banali naye banayenda kufika mumzinda. Banafia pafupi namuzinda nakumanga misasa kumbali yaku mpoto kwa Ai, Manje panali cigwa pakati pao na Ai. 12 Anatenga bamuna a Faivi (5) sazande na kui ka mobisika kumbali ya ku mazulo kwa muzinda pakati ka Beteli na Ai. 13 banaimika ba silikali bonse, gulu ya nkhondo ikulu kumpoto kumbali kwa muzinda, na olonda kumbali yakumazulo kwa mzinda. Yoswa anagona mucigwa usiku uja. 14 Zinacita pamene mfumu ya ku Ai inacibona, na gulu yake yankhondo inauka kuseni nakucoka kuyenda kumenya Israyeli pamalo pena yamene kuthila mucigwa ca mumana wa Yolodani, sanazibe kuti baja bobisama banali kuyembekeza kumenyela kumbuyo kwa muzinda. 15 Yoswa na Israyeli bonse banalekelela kuti bagonjesewe pamenso pao, na kuthabila ku cipululi. 16 Onse bantu banali mu mzinda banaitaniwa kuti ba pepeke, ndipo banapepeka Yoswa nakucosewako ku muzinda. 17 Kulibe munthu alibonse anasalila mu Ai na Beteli amene anayenda kupepeka Israyeli. Banasiya muzi kopanda aliyense pamene banapepeka Israyeli. 18 Yehova anakamba kuli Yoswa, ''penyesa mkondo uyo uli mumanja yako ku, popeza nizapasa Ai mumanja mwako.'' Yoswa anacosa mukundo unali manja mwake kupenyesa ku muzinda. 19 Basilikali bobisama msanga banathmanga kucoka mumalo yao pamene anatambasula kwa nja kwake. Banathamanga nakungena mumuzi na kuutenga. mwamsanga bana shoka muzi. 20 Bamuna baku Ai banapindamuka hakuyangana ku mbuyo. Banabona cusi kucoka mumzinda ciyenda mumwamba, pamenepo banakanga kuthabila ukukapena uko. popeza basilikali ba Israyeli bamene banathabila mucipululu manje banabwelela kukumana nabaja benza kuba pepeka. 21 Pamene Yoswa na Israyeli banaona kuti bobisama banatenga muzinda na cusi ciyenda mwamba banabwelela nakupaya bamuna ba ku Ai. 22 Bena banatuluka mumuzinda kuba menya, kuti ibo banagwiliwa pakati, na Israyeli pakati, bena kumbali na mbali ija. Israyeli anameya bamuna baku Ai palibe anapulumuka kapeka kuthaba. 23 Banasunga mfumu ya ku Ai, wamene banagwira wamoya na ku muleta kuli Yoswa. 24 Pamene Israyeli anasiliza kupaya bonse bokhala mu Ai mumunda pifupi nacipululu kwamene anaba pepekela, napamene bonse, kufikila wosilizila, anagwa na lupanga Israyeli bonse anabwelela ku Ai, Banamenya Ai na lupanga. 25 Bonse banagwa siku ija, bonse bamuna na bakazi, benze tyovu sauzandi (12), bonse banthu ba mv Ai. 26 Yoswa sanabweze kwanja kwake kwamene anatambasula pamene anagwila mukondo, paka anabonongelatu banthu bonse ba mu Ai 27 Israyeli anatenga vobeta navtenga kucoka mumzinda, monga mwamene Yehova anabalamulila Yoswa. 28 Yoswa anashoka Ai na kuusandusa muunda wamavuto muyaya. Nimalo yosiyiwa kufika lelo 29 Anapaci,a mfumu yaku Ai pamtengo paka mazulo. Pamene zuba yenze kungena, Yoswa anapa lamulo na kuseluse thupi yamfumu nakuika pasogolo pakhomo ya muzinda. pamenepo banaikapo miyala ikulu ya mbiri pamwamba pake. Yaja miyala yalipo kufika lelo. 30 Pamene Yoswa anamangila Yehova gowa, mulungu wa Israyeli, pa pili ya Ebal, 31 Monga mwamene Mose mutumiki wa Yehova analamulila bana ba Israyeli, mwamene cinalembewela mubuku yacilamulo ca Mose.'' Guwa kucoka kumiyala yosajubiwa, pamene kulibe anapangilapo cisulo cansimbu,'' Anapeleka nsembe zo pseleza paguwa kuli Yehova, nakupeleka nsembe zamtendele. 32 Pamenepo mumenso ya bana ba Israyeli, malemba pamiyala cisanzo calamulo ya mose. 33 Israyeli bonse, bakulu bao, bobayang'anila, na boweliza banaimilila kumbali zonse zibili zalikasa pamenso ya bansembe na Alevi bananyamula likasa yacipangano ca Yehova - mlendo na bobadwila muziko bena pali beve banaimilila kusogolo kwa phili ya Gelezimu na bena kusogolo kwa phili ya Ebal. Bana ba Israyeli, monga mwamene Mose mtumiki a mulungu anabalamulila poyamba. 34 Pambuyo pake, Yoswa anabelenga mau yonse ya cilamulo, madaliso na matembelelo, monga mwamene banayalembela mubuku ya lamulo. 35 Kunalibe mau yaliyonse yamozi kuli vonse Mose malamulila vamene yoswa sanabelenge kusogolo kwa gulu ya Israyeli, kufakilako bazimai, bana bang'ono nabalendo banakhala pakati pao.