Mutu 34

1 Elihu anapitiriza kulankhula kuti: 2 “Tamverani mawu anga, anzeru inu, ndimvereni, inu akudziwa. 3 Pakuti khutu liyesa mawu, monga m'kamwa mulawa kulawa. 4 Tiyeni tisankhe tokha chomwe chiri cholungama: tizindikire pakati pathu chomwe chili chabwino. 5 Pakuti Yobu anati, 'Ine ndine wolungama, koma Mulungu wandilanda. 6 Kaya ndili ndi ufulu wotani, ndimaonedwa kuti ndine wabodza. Chilonda changa sichitha, ngakhale ndilibe uchimo. ' 7 Ndi munthu uti amene angafanane ndi Yobu, amene amamwa zopanda pake ngati madzi, 8 amene amayenda m thegulu la anthu ochita zoyipa, ndipo amayenda ndi anthu oyipa? 9 Pakuti iye anati, 'Sizothandiza kwa munthu kusangalala ndi zinthu zimene Mulungu amafuna.' 10 Chifukwa chake, ndimvereni, inu anzeru: kuti kutari ndi Mulungu kuchita zoyipa; kukhale kutali ndi Wamphamvuyonse kuchita tchimo. 11 Pakuti amabwezera ntchito ya munthu; amachititsa munthu aliyense kubwezera mphotho ya njira zake. 12 Ndithudi, Mulungu sachita choipa chilichonse, ndipo Wamphamvuyonse sapotoza chiweruzo. 13 Ndani anamuika woyang'anira dziko lapansi? Ndani adaika dziko lonse pansi pake? 14 Ngati angakhazikitse zolinga zake pa iye yekha, ndipo ngati angabwezeretse kwa iye mzimu wake ndi mpweya wake, 15 pamenepo anthu onse adzawonongeka pamodzi; anthu adzabwerera kufumbi. 16 Ngati tsopano muli ndi chidziwitso, mverani ichi; mverani mawu anga. 17 Kodi amene amadana ndi chilungamo angalamulire? Kodi muweruza Mulungu, wolungama ndi wamphamvu? 18 Mulungu amene amati kwa mfumu, 'Inu ndinu oipa,' kapena amene munena kwa anthu olemekezeka kuti, 'Ndinu oipa'? 19 Mulungu, amene samakondera atsogoleri ndipo salemekeza anthu olemera kuposa osauka, chifukwa onse ndi ntchito ya manja ake. 20 Adzafa m'kamphindi, pakati pausiku anthu adzagwedezeka, nachoka; anthu amphamvu adzatengedwa, koma osati ndi manja a munthu. 21 Pakuti maso a Mulungu amayang'ana njira za munthu; amapenya mayendedwe ake onse. 22 Palibe mdima, kapena mdima wandiweyani kumene ochita zosalungama angabisalire. 23 Pakuti Mulungu safunikiranso kusanthula munthu; palibe chifukwa choti munthu aliyense apite kukamuweruza. 24 Amaphwanyaphwanya amuna amphamvu chifukwa cha njira zawo zosafunikira kufufuzidwa; amaika ena m'malo awo. 25 Mwa ichi akudziwa zochita zawo; agwetsa anthuwa usiku; awonongedwa. 26 Poyera ena, amawapha chifukwa cha zoyipa zawo ngati zigawenga 27 chifukwa adasiya kumutsata ndikukana kuvomereza njira zake zonse. 28 Mwanjira iyi, adafuulira kulira kwa anthu osauka kudza kwa iye; anamva kulira kwa anthu ovutika. 29 Akangokhala chete, ndani angamuweruze? Ngati abisa nkhope yake, ndani angamuzindikire? Iye amalamulira pa dziko ndi anthu ena, 30 kuti munthu wosapembedza asalamulire, kuti pasakhale wina wokopa anthu. 31 Munthu wina akauza Mulungu kuti, 'Ine ndachimwa, koma sindichimwanso; 32 ndiphunzitseni zomwe sindingathe kuziona; Ndachita tchimo, koma sindidzachitanso. ' 33 Kodi mukuganiza kuti Mulungu adzalanga tchimo la munthu ameneyo, popeza simukukonda zomwe Mulungu amachita? Muyenera kusankha, osati ine. Chifukwa chake nenani zomwe mukudziwa. 34 Anthu anzeru adzanena ndi ine, inde, yense wanzeru wondimva Ine adzati, 35 Yobu alankhula osadziwa; Mawu ake alibe nzeru. ' 36 Zikanakhala kuti Yobu anaimbidwa mlandu ngakhale pa nkhani zazing’ono za mlandu wake chifukwa cholankhula ngati anthu oipa. 37 Pakuti akuwonjezera kupanduka pa tchimo lake; akuwomba m'manja potonza pakati pathu; Akuunjika mawu otsutsana ndi Mulungu. "