MUTU 1

1 Kunali mwamuna mumalo ya Uzi wamene zina yake inali Yobo; ndipo Yobo analibe mulandu ndipo owongoka, wamene anali kuyopa mulungu nakutaya voipa. 2 kuli eve kunabadwa bana bamuna 7 na bana bakazi batatu. 3 Anali na mbelele 7,000, macamelo 3,000, 500 ma peyala ya ng'ombe na mabulu 500 na banchito bambili maningi. Anali mwamuna wamene anali wopambana pali bantu bonse bakumaba. 4 Pasiku yotumikila ya mwana wake umozi, anali kupanga madyelelo mu nyumba yake. Banali kutuma nakuitana balongo bao batatu kuti badye na kumwa nabeve. 5 Pamene ma siku yama dyelelo yanasila, Yobo anali kubaitana naku bayelesa. Anali ku uka kuseni maningi naku peleka nsembe zo shoka za mwana wake aliense, chifukwa analikukamba,'' chingankale kuti bana banga bachimwa na kutembelela mulungu mumitima yao.'' Yobo anali kuchita ivi ntawi zonse. 6 Mwaicho inali siku yamene bana bamulungu banabwela kuonekela pa menso ya Yehova. Satana naye anabwela na beve. 7 Yehova anakamba kuli satana,''Nikuti kwamene wachokela?'' Satana anayanka Yehova nakukamba kuti,'' kuyenda chiyende yende paziko yapansi, kuchokela kuyenda pasogolo na pambuyo pake. 8 Yehova anakamba kuli satana,Wamuona wanchito wanga Yobo? Pakuti kulibe ali monga eve pa ziko yapansi mwamuna alibe mulandu ndipo owongoka, uyo wamene ama yopa mulungu na kusiya voipa.'' 9 Ndipo satana anayanka Yehova nakukamba kuti, Kodi Yobo amayopa mulungu palibe chifukwa? 10 Siunaike chochinga momuzungulukila, mozungulukila nyumba yake, na mozunguluka vintu vake vonse mubali monse? Wadalisa nchito za manja yake,na viweto vake vafikila ku malo yonse. 11 Koma manje tambusula kwanja kwako nakugwila vonse vame ali navo, ndipo uwone ngati saza kutembelela pamenso yako.'' 12 Yehova anakamba kuli satana kuti, ''Onani,vonse vamene ali navo vili mumanja yako. Koma kuli eve manja yako yasamugwile.'' Ndipo satana anayenda nakuchoka pa menso ya Yehova. 13 Chinachitika kuti pa siku ina, bana bake bamuna na bakazi banali kudya na kumwa vinyu mu nyumba ya bale wao mukulu. 14 Wotumimiwa anabwela kuli Yobo nakukamba kuti,'' ng'ombe zinali kulima na mabulu yanali kudya pambali pa zeve. 15 Ndipo ma sabiyeni yanizigwela nakuzitenga. Koma kuli banchito, babagwesa na mapanga. Ine neka nataba kubwela kukuuza. 16 Pamene akachiali kukamba, winangu naeve anabwela nakukamba kuti, '' Mulilo wa mulungu unagwa kuchokela kumwamba nakushoka mbelele na banchito. Ine neka nataba kubwela kukuuza.'' 17 Pamene akachili kukamba, wenangu nafuti anabwela nakukamba kuti, ''Ba chalideni banapanga ma gulu yatatu, nakukata ma kamelo, nakuyenda nayo. Koma banchito, babagwesa na panga.Ine neka nabataba kubwela kukuuza.'' 18 Pamene akachili kukamba, wenangu anabwela nakukamba kuti, ''Bana bako bamuna naba kazi banali kudaya na kumwa vinyu munyumba yabale wao mukulu. 19 Mpepo yampavwu inabwela kuchokela kuchipululu naku fimba muma kona yali 4 yanyumba. Inagwela pali bana bang'ono, ndipo bafa.'' 22 Ndipo Yobo ananyamuka, nakung'amba mukanjo wake, nakugela mutu wake, nakugona moyangana pansi, nakupempela kuli mulungu. 21 Anakamba,'' nina osavala pamene ninachoka mumala yabamai banga,ndipo nizankala osavalapamene nizabwelelamo. Ni Yehova wamene amapasa, ndipo ni Yehova wamene atenga. Zina ya Yehova idalisike.'' 20 Muli nkani iyi yonse, Yobo sanachimwe, kapena kunamizila Yehova pali kuchita voipa.