Mutu 45

1 Ndipo Yosefe anakangiwa kuzilesa kuti asalile pa menso pa banchito bake. Anakamba mopunda, " Bonse banisiye," panalibe wanchito aliyense pamene Yosefe anaziulula kuli ba bale bake. 2 Analila na chongo, ndipo Aigupto bananvela, na nyumba ya Farao inanvela. 3 Yosefe anati kuli ba bale bake, " Ine ndine Yosefe. Ushe batate banga bakali moyo?" Koma ba bale bake sibanamuyake, chifukwa banali namata pamenso pake. 4 Ndipo Yosefe anati uli ba bale bake, "bwelani pafupi naine, napapata." Banabwela pafupi. Anati ndine Yosefe mubale wanu, wamene muna gulisa ku Igupto. 5 Osazibalisa na kuzikalipila mweka kuti munaningulisa ine kuno, chifukwa Mulungu ananituma ine pasongolo panu nikapulumuse umoyo. 6 Pa zaka zibili izi kwa nkhala njala mumalo ndipo kulinso zaka 5 pamene sikuzankhala kulima kapena kukolola. 7 Mulungu ananituma pasongolo panu kuti akakusungeni monga onkhala pa ziko yapansi ndipo kukusungani naumoyo ndi kumasulidwa kukulu. 8 Sopano, sindimwe munanituma kuno koma Mulungu, ananifaka kunkhala tate wake wa Farao, bwana wa nyumba yake yonse, ndi olamulila malo yonse ya Igupto. 9 Yendesani ndipo muyende kuli batate banga nakubauza kuti, ichi ndiye chamene mwana wanu Yosefe akamba, " Mulungu anipanga ine kunkhala bwana mu Igupto monse. Bwelani kwa ine, ndipo musa chedwe. 10 Muzankhala mu malo ya Goseni, ndipo muzankhala pafupi naine, imwe na bana banu na bazukulu banu, na nkosa na ng'ombe, na vonse vamene muli navo. 11 Nizakupasani imwe kuja, chifukwa kuli zaka 5 zanjala, kuti musabwele kuumpawi, imwe nyumba yanu, na vonse muli navo." 12 Onani, menso yanu yaona, na menso ya mubale wanga Benjamini, kuti ndi kamwa kanga kamene kakamba kwa imwe. 13 Mukabauze batate banga pa ulemele wanga wonse mu Igupto na vonse vamene mwaona. Muyayendesa na kubwelesa batate banga kuno." 14 Anakumbatila mu'bale wake Benjamini mukosi na kulila, ndi Benjamini analilila mumu kosi wake. 15 Anapyompyona ba bale bake bonse na kulila kuchoka apo ba bake bana kamba naye. 16 Nkhani ya ichi chintu inauzidwa kunyumba kwa Farao: " Ba baleba Yosefe babwela chinakondwelesa Farao na ba nchito bake kwambili. 17 Farao anati Yosefe, " Uza ba bale bako chitani ichi: Longani pa nyuma zanu ndipo muyende ku ziko ya Kanani. 18 Tengani batate banu na banja ndipo mubwele kwa ine. Nizakupasani vabwino va mu malo la Igupto, ndipo muzadya zonona zamu ziko.' 19 Manje mwauzidwa, 'Chitani ichi, tengani kochikali ku choka mu ziko la Igupto kwa bana banu na ba kazi banu. Tengani batate banu na kubwela. 20 Musaganiza pa vintu vamene muli navo, chifukwa vabwino va ziko ya Igupto nivanu.'" 21 Bana ba Israeli bana chita zamene izo. Yosefe anabapasa vi kochikali, monga mwamene anakambila Farao. Ndipo anabapasa vakudya va munjila. 22 Kuli ali bonse anapasa vovala vinangu koma kuli Benjamini anamupasa siliva ili fili handilendi na vovala vili fivi. 23 Kuli ba tate bake anatuma ivi: Ba bulu bali teni wozula ndi vintu vabwino vaku Igupto; ndi mabulu bakazi bali teni, banatenga tilingu, buledi ndi vinangu vofunika va batate bake vamunjila. 24 Ndipo anabatuma ba bale bake kuti ba yambepo. Anabauza kuti, " Muone kuti musayambane munjila." 25 Bana choka mu Igupto nakubwela ku ziko la Kanani, kwa Yakobo tate wabo. 26 Banamu uza kuti, " Yosefe akali moyo, ndipo wamene alamulila mu ziko yonse ya Igupto." Mutima wake unadabwa,, chifukwa sana kulupilile vamene bana mu uza. 27 Bana mu uza mau yonse ya Yosefe yamene ana bauza. Pamene yakobo anaona ma kochikali yamene Yosefe anatuma kumutengelapo, muzimu wa Yakobo tate wawo unauka. 28 Israeli anati, " Zakwana. Yosefe mwana wanga akali moyo. Nizayenda mukumuona nikalibe kufa.