Mutu 37

1 Yakobo anankala mu malo ya Kanani, mwamene anankalamo batate bake. 2 Ivi ndiye vinachitika pa umoyo wa Yakobo, Yosefe, wamene anali munyamata mufana wa zaka seventini, anali kulonda vinyama nazibale bake. Anali na bana ba Bila na bana ba Zelipa, bakazi ba batate bake. Yosefe anali kubaletela lipoti yoyipa kuli tate wawo. 3 Koma manje Isilayeli anakonda Yosefe manigni kupambana na bana bake bamuna bonse chifukwa ndiye mwana anabadwa Yakobo atakalamba pa bana bamuna bonse. Anamupangila chovala chabwino maningi. 4 Babale bake banaona kuti batate babo amukonda maningi kuchila na pa bana bonse. Anamuzonda andipo sanalikukamba naye bwino mwa chifundo. 5 Yosefe analota maloto, naku uza babale bake viloto vamene ivi. Banamuzondelako maningi. 6 Anakamba kuli benve kuti, Napapata nvelani maloto yanga yamene na lota. 7 Onani, tinali kumanga mitolo ya vamumunda ndipo onani, mutlolwanga unayamuka nakuyimilila kuyanga kumwamba, ndipo onani, mitolo yanu inabwela mumbali zonse nakubelamila mutolo yanga." 8 Babululu bake banakamba kuli enve kuti, "Zo'ona uzatilamulila ise? uzatisogolela zo'ona ise? Banamuzondelako enve chifukwa chamaloto yake na mau. 9 Analota maloto yenangu naku uzako babale bake. Anakamba kuti, "Onani, nenze nalota loto inangu: Zuba na mwezi na nyenyezi zili leveni zinali kugwadila ine." 10 Anayenda kukamba maloto kuli batate bake chimozi mozi mwamene anauzila babale bake, ndipo batate bake anamukalipila. Anakamba kuli enve kuti, " namaloto yamu tundu bwanji aya yamene walota? ushe vizakachitika zo'ona kuti bamai bako naine naba bale bako tizabwela naku kugwadila pansi kuli iwe? 11 Abale bake banamuchitlila jelasi, koma batate bake banasungila iyi nkani mumutima mwao. 12 Ba bale bake banayenda kukadyesela vinyama va batate babo ku Shekemu. 13 Isilayeli anakamba kuli Yosefe kuti, "kodi azibale bako sibanyende kudyesa vinyama ku Shekemu? Bwela ndipo nizakutuma kuli benve." Yosefe anakamba kuli batate bake, "Ndine okonzeka." 14 Anakamba kuli enve kuti, "Yenda manje, ukaone ngati vibayendela bwino benve navi nyama, ndipo uniletele mau." Ndipo Yakobo anamutuma kuchokela ku vale ya Hebroni ndipo Yosefe anayenda ku Shekemu. 15 Muntu winangu anamupeza Yosefe ali kuyenda musanga. Mwamuna uja anamufunsa "Usakila chani?" 16 Yosefe anayanka kuti nisakila azibale anga, niuzeni, nisakila zaiblae anga, miuzeni napapata, kwamene balikudyesela vinyama. 17 Mwamuna uja anati, "Banachokako kuno, ndaba na banvela bakamba kuti, tiyeni ku Dotani." Yosefe anaba konkamo ba bale bake bapeza ku Dotani. 18 Banaona bakali kutali, ndipo bakalibe kufika pafupi nabenve, bana pangana mwachiwembu kuti amupaye. 19 Ba bale bake banakambisana kuti, "Onani, Uyu wamaloto wabwera pafupi. 20 Bwelani manje apa, chifukwa chake, tiyeni timupaye timuponye mu umozi mu mugodi ilikuno. Tizakamba kuti, 'Chinyama chamusanga chinamudya. ' Tizaona vamene maloto yake yazasanduka." 21 Rubeni anamvela iyi nkani nakumupulumusa mumanja mwao. Anakmba kuti, Tisamu paye." 22 Rubeni anakamba kuli benve kuti, "Osakesa magazi muponyeni mumu godi uyu uli kuno kusanga, koma asamu kumyako kwanja, "pofuna kuti angamupulumuse kumuchosa mumanja mwao nakuyenda kumupeleka kumubweza kuli batate bake. 23 Chinachitika kuti pamene Yosefe anafika pali bazibale bake, banamu vula chovala chake chokongola. 24 Banamutenga nakumuponya mumugodi munalibe chintu, ndipo munalibe manzi mukati. 25 Bana nkala pansi kuti badye buledi. Bananyamula menso yabo nakuona, ndipo, onani, kunali kalavani yama Ishamealiti inali kubwela kuchokela ku Giliyadi, nama kamelo yabo yonyamula masipayisi na balami na mure. Banali paulendo bopeleka iyi katundu ku Iguputo. 26 Yuda anakamba kuti kuli ba bale bake, "Pali pindu yabwanji ngati tizamupaya mubale watu nakubisa magazi yake? 27 Bwelani, ndipo tiyeni timugulise kuli ma Ishiamyeliti ndipo tisakumyepo manja yatu pali enve. Pakuti nimubale watu, magazi yatu, " Ba bale bake banamunvelela iyi. 28 Mamechanti baku Midiyani banapitila pafupi. Ba bale bake banamudonsa Yosefe nakumunyamula kumuchosa mumugodi. Banamugulisa Yosefe kuli ma Ishimayeleti pa mutengo wa twenti ndalama za siliva. ndipo ma Ishimayeliti anamunyamula Yosefe kuyenda naye ku Iguputo. 29 Rubeni anabwelelapo pamugodi, ndipo onani, Yosefe analimo mumugoidi. 30 Iye anang'amba vovala vake. Anabwelela kuli bazibale bake nakukamba kuti munyamata salimo! ndipo ine nizayenda kuti?" 31 Banapaya mbuzi naku tenga malaya ya Yosefe nakuya sunsika mu magazi. 32 Pamene banaleta chija chovala kuli batate babo nakukamba kuti," Tapeza ichi. Tapapata chiyanganeni ngati ni chovala chamwana wanu kapena olo sichamene." 33 Yakobo anachiziba nakukamba kuti, "Nichoavala cha mwana wanga mwamuna. Chinyama chamusanga chamudya. Yosefe akazuliwa zo'ona mumapisi na chinyama." 34 Yakobo anang'amba vovala vake naku vala 36 chovala chamsaka mumusana. Analila mwana wake mwamuna masiku yambili. 35 Bonse bana bake bamuna na bakazi bananyamuka kumu tandiza kulila momupepesa, koma anakana kumuchita kamfoti. Anakamba kuti, "Zo'ona nizayenda ku Shilo nikalikulila mwana wanga." Batate nake banalila mokuwa kamba ka enve. Ma Midiyanaiti yanamugulisa mu Iguputo kuli Potifa mu ofisala wa Farao, mukulu wama bodigadi.