Mutu 33

1 Yakobo onayangana kumwamba, onani, Esau akubwela, pamodzi naive anali amuna ake 400. Yakobo anabagawa bana bake pakati pa ba leya, ba rakele ndi anchito akazi abili. 2 Ndipo anaika anchito na bana bawo kiutsogolo, kukonkapo anali leya na bana bake na kukonkapo anali Rakele na Yosefe kumbuyo kwa bonse. 3 Iye mwine anayenda patsogolo pa bonse. Iye anagwanda pansi ka 7, kufikila anafika pafupi na mbale wake. 4 Esau anamutamangila iye, na kumukumatila, na kumulandila ndi kumufyofyonta. Ndipo iwo analila. 5 pamene Esau anayangana ku sogolo, anaona azimai ndi bana. Iye anakamba, " Nindani awa banthu amene bali na iwe? " Yakobo anakamba, " Aba ni bana amene Mulungu mwacisomo cake anapasiwa na wancito wanu." 6 Ndipo banchito akazi banafika pamodzi ndi bana bawo ndipo banagwanda pansi. 7 Wokonkhapo anali Leya ndi bana bake anafika ndi kukwanda pasi. Posilizila Yosefe na Rakele ana bwela na kugwanda. 8 Esau anakamba, " Utanthauza ciani pa banthu wonse aba bambili nakumana nao?" Yakobo anakamba, " Kuti nipeze mwayi pameso pa bwana wanga." 9 Esau anakamba, " Nili nazo zokwanila, mbale wanga. Zisungele zonse zamene ulinazo." 10 Yakobo anakamba, " Yai, napapata, Ngati napeza mwayi pa menso panu, nipempa kuti mulandile mpaso iyi yofumila m'manja yanga. 200 nadi naona pa maso pano, cili nga nikuona pa maso pa Mulungu, ndipo mwani landila ine. 11 Napapata landilani mpaso yanga yamene nakubweleselani ine, cifukwa Mulungu wacita naine mwa cisomo, ndipo ndili nazo zokwanila," Pamene Yakobo anamupapatila, Esau analandila mpaso ija. 12 Ndipo Esau anakamba, "Tiyeni tiyambepo kuyenda, ine nizakhala pa songolo panu." 13 Yakobo anamu uza iye, " Mbuye wanga zibani ici kuti bana nibang'ono, ndi mbelele ndi ng'ombe zinyonsha tubana. Ngati tizayenda mwa mpavu cukanga siku imodzi cabe zibeto zizafa. 14 Napapata lekani bwana ayende patsongolo pa kapolo wanu. Nizayenda pangono pang'ono, ngani mwazibeto zamene zili ku songolo, ndi monga bana, kufikila tifike kwa bwana wanga ku Seiri." 15 Esau anakamba, " Lekani nikusiyileni amuna banga amene bali na ine" Koma Yakobo anayankha, " Ciani mzacitila izo? Lekani nipeze mwayi pamanso ya bwana wanga." 16 Ndipo Esau pa siku ija anayambapo ulendo wake kupita ku Seiri. 17 Yakobo anayenda ku sokoti, kukazimangila iye mwine nyumba na makolo ya zibeto zake. Ndipo zina la malo ndi Sokoti. 18 Pamene Yakobo anacoka kufumila ku padamu Aramu, anafika bwino ku mzinda wa Shekemu, malo yopezeka mu Kenani anaphumulila pafupi ndi mzinda. 19 Ndipo anagula malo pamene anamangila Hema kucokela ku mwana wa Hamo, tate wa Shekemu, ndi mutengo wa Hundriredi ziduswa za siliva. 20 Kuja anamanga guwa ndikuipatsa zina kuti Eli Elone Isilayeli.