Mutu 22

1 Pamene ivi vinapita Mulungu anayesa Abrahamu. Anamu uza kuti, "Abrahamu!" Abrahamu anayanka kuti, "Ine nili pano." 2 Mulungu anakamba kuti, "Mutenge mwana wako, mwana mwamuna wako eka, wamene ukonda, Isaki, uyende ku malo ya Molaya. Umupase ankale nsembe yoshoka pa pili imozi yakuja, yamene nizaku uza." 3 Mwa ichi Abrahamu anaima kuseni-seni, anakwela bulu yake, anatenga banyamata babili bang'ono pamozi na eve, na Isaki mwana wake. Anatyola mitengo zopelekelapo nsembe, nanyamuka ulendo kuyenda kumalo kwamene Mulungu anamu uza. 4 Pa siku yachitatu Abrahamu anaimya menso nakuyaona malo pataliko. 5 Abrahamu anauza banyamata bake kuti, "Lindilani pamene pano na bulu, ine na munyamata tiyenda apo. Tizapembeza naku bwela futi kuli imwe." 6 Abrahamu anakonza nkuni za nsembe naku ikapo mwana wake Isaki. Ananyamula kumanja mulilo na lupanga; ndipo bana enda pamozi. 7 Isaki anauza Abrahamu tate wake kuti, "Batate banga," ndipo banamuyanka kuti, "Ine pano, mwana wanga." Anakamba kuti, "Onani, uyu apa mulilo na nkuni, manje nanga kamwana ka nkosa kopeleka nsembe kali kuti?" 8 Abrahamu anayanka kuti, "Mulungu azapeleka eka mwana wankosa wa nsembe yo ocha, mwana wanga." Mwamene umo banaenda, bonse babili pamozi. 9 Pamene banafika pamalo yamene Mulungu anamuwuzapo eve, Abrahamu anamanga guwa yansembe pamene apo na kuyikapo nkuni zija. Pamene apo anamangilila Isaki mwana wake, nakumugoneka paguwa yansembe, pamwamba pa nkuni. 10 Abrahamu anatambasula kwanja kwake nakutenga mupeni kuti apaye mwana wake. 11 Ndipo mungelo wa Yehova anamuitana eve kuchokera kumwamba kukamba kuti, "Abrahamu, Abrahamu!" ndipo anati, Ine pano. 12 Eve anakamba kuti, "Usaike kwanja yako pali munyamata uyo, kapena kumuchita chilichonse choipa, chifukwa manje naziba kuti iwe uyopa Mulungu, popeza kuti sunanikanile ine mwana wako, mwamuna wobadwamo eka." 13 Abulahamu anaimya menso yake ndipo, onani, kumbuyo kwake kunali nkosa yamphongo yamene inagwiliwa na nsengo zake. Abulahamu anaenda kukaitenga nkhosa yamene ija na kuipeleka monga nsembe yopsereza mumalo mwa mwana wake. 14 Ndipo Abrahamu anaitana malo yamene yaja kuti ni "Yehova azapeleka", kufikila na lelo, "Pamwamba pa lupili ya Yehova vizapasiwa. 15 Mungelo wa Yehova anaitananso Abrahamu kachibili kuchokera kumwamba, 16 naku kamba kuti- “Yehova akamba kuti, Ine nalapa pa ine kuti chifukwa wachita chintu chamene ichi, kosanikanila mwana wako mwamuna umozi eka, 17 nizakudalisa Nizachulukisa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba, na monga muchenga wa mumbali mwa nyanja; ndipo mbewu zako zizatenga chipata cha adani awo. 18 Kupitila mwa mbewu yako, mitundu zonse zapa ziko yapansi zizadalisika, chifukwa wamvera mawu yanga.” 19 Ndipo Abrahamu anabwelela kuli banyamata bake, ndipo anachoka nakuyenda bonse pamozi ku Biyasheba, ndipo eve anankala ku Biyasheba. 20 Chinachitika kuti pamene ivi vinapita banamuuza Abrahamu kuti, Milika nayeve anabala bana kuli mubale wako Naholi. 21 Aba banali mwana wake woyamba Uzi, mubale wake Buzi, Kemuweli anabala Alamu, 22 Kesedi, Hazo, Piludashi, Yidilafu na Betuele. 23 Betuele anabala Rabeka. Aba ndiye bana basanu na batatu bamene Milka anamubalira Naholi mubale wa Abrahamu. 24 Mukazi wake wamung'ono, dzina yake Reuma, anaba nafuti Teba, Gahamu, Tahasi na Maaka.