Mutu 20

1 Abrahamu anacokako kuja kupita ku malo ya Nagev, ndipo anankhala pakati padesi na suri. Enze mulendo wonkhala mu Gerari. 2 Abrahamu anakamba pali Sara mkazi wake, " Uyu ninabadwa naye." Abimeleki mfumu ya Gerari anaitana Sara na kumtenga. 3 Koma Mulungu anabwela kwa Abimeleki mu maloto usiku, na kuti kwa eve, " Ona, ndiwe munthu wokufa cifukwa ca mkazi wamene watenga, pakuti ni mkazi wa munthu." 4 Manje Abimeleki sanabwele pafupi na eve ndipo anakamba kuti, "Ambuye, munga paye ziko yalungama? 5 Sanakambe eve eka kwa ine, ' ninabadwa naye, 'Nacita ici mwa ulemu wa mtima wangu na kupanda cifukwa kwa manja banga." 6 Ndipo Mulungu anakamba kuti kwa eve m'maloto, " Ee, niziba naine kuti mu ulemu wa mtima wako wacita ici, ndipo naine ninakulesa kunicimwila. Mwaici sininakuvomeleze iwe kuti umugwire. 7 Mwaici, bweza makazi wa munthu, pakuti ni mneneri. Azakupemphelera, ndipo uzankhala moyo. Koma ngati sumubwezela, ziba kuti iwe na ose amene uli nao zoona muzafa." 8 Abimeleki ananyamuka kuseni seni na kuziitanila banhito. Anabauza ivi vinthu vonse kwa beve, na banthu banacit mantha. 9 Ndipo Abimeleki anaitana Abrahamu na kukamba kuti, " Nicani camene wacita kwa ise? Nakucimwila bwanji, kuti wanibwelesela ine ufumu wanga cimo ikulu? Wanicitila camene siwenzofunika kucita." 10 Abimeleki anakamba kuti kwa Abrahamu, " Unaona cani kuti ucite ici cinthu?" 11 Abrahamu anakamba kuti, " Cifukwa ninaganiza, ' zoona mulibe kuyopa mulungu mu malo muno ndipo bazanipaya cifukwa ca mkazi wanga.' 12 Pakuti, zoona ninabadwa naye, ni mwana mkazi wa batate banga, koma osati mwana mkazi wa amai banga; ndipo anankhala mkazi wanga. 13 Pamene Mulungu ananilengesa kucoka pa nyumba ya batate banga na kuyenda kucoka ku malo aba kupita pa malo pena. Ninakamba kuti kwa eve, ' ufanika unilangize kukhulupilika kwako monga mkazi wanga: Pamalo paliponse pamene tizayenda, ukambe za ine, " Ninabadwa naye." 14 Ndipo Ambimeleki anatenga mbelele na ng'ombe, na akapolo bamuna na bakazi, na kubapeleka kwa Abrahamu. Ndipo anambwezela Sara, mkazi wa Abrahamu, kwa eve. 15 Abimeleki anakamba kuti, " Ona, malo bangaali m'manja mwako. Nkhala paliponse pamene pazakukondwelesa." 16 Kwa Sara anakamba kuti, " Ona, napasa wobadwa naye wako ma sauzande ya silive. Ici nikuvinikila zolakwa pali iwe mu menso mwa onse bali na iwe, na pamenso pa aliyense, wapangiwa wonkhalilatu wolungama." 17 Ndipo Abrahamu anapemphela kwa Mulungu, ndipo Mulungu anapolesa Abimeleki, mkazi wake, na bakapolo bake bakazi kuti bakwanise kunkhale na bana. 18 Pakuti Yehova analengesa onse bakazi ba mnyumba mwa Abimeleki bankhaliletu osabala, cifukwa ca Sara, mkazi wa Abrahamu.