Mutu 4

1 Yesu anatengewa na Muzimu kuyenda mu chipululu kuti akayesewe na mudyelekezi. 2 Pamene anasala chakudya muzuba na usiku masiku yokwanila 40, anamvela njala. 3 Eve oyesa anabwela naku muuza kuti, "Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, uza izi myala kuti zisanduke kunkala mukate." 4 Koma Yesu anamuyanka kuti, "chinalembewa kuti, 'Muntu sazankala na moyo kamba ka chakudya cheka, koma na mau yali yonse yamene yachokela mukamwa mwa Mulungu.'" 5 Pamene apo mudyelekezi anamutenga kuyenda naye mu muzinda woyela nakumuika pa mwamba mwamba pa tempele, 6 naku kumuuza kuti, "Ngati ndiwe Mwana wa Mulungu, ziponye pansi, chifukwa nicholembewa kuti, 'Eve azauza bangelo Bake kuti bakusamalile Iwe,'komanso, 'Bazakunyamula mumanja yabo, kuti usamenye kwendo Yako pa mwala.'" 7 Yesu anakamba kuli eve, "Futi chinalembewa kuti, 'Usayese Ambuye Mulungu wako.'" 8 Futi, mudyelekezi anamutenga pamwamba pa lupili ikulu nakumulangiza ma ufumu yonse yapa ziko yonse pamozi na ulemelelo wao. 9 Anamuuza kuti, "Vonse ivi vintu nizakupasa Iwe, ngati uzagwada pansi naku nipembeza ine." 10 Ndipo Yesu anamuuza kuti, "Chokapo apa iwe, Satana! Chifukwa chinalembewa kuti, 'Uzalumbila Ambuye Mulungu wako, komanso eve eka ndiye wamene muzatumikila.'" 11 Pamene apo mudyelekezi anamusiya, ndipo onani, bangeli banabwela naku mutumikila. 12 Manje pamene Yesu anamvela kuti Yohane anagwiliwa, anabwelela kumalo ya ku Galileya. 13 Anachokako ku Nazaleti naku yenda kukankala ku Kapenamu, malo yamene yali ku nyanja ya Galileya kumalo yaku Zebuluni na Nafutali. 14 Ichi chinachitika kuti vamene anakamba muneneli Yesaya vikwanilisike, 15 "Malo ya Zebuluni na malo ya Nafutali, kuyangana ku nyanja, kupitilila Yodani, Galileya malo yaba Kunja! 16 Bantu bamene bankala mumudima baona nchinyali chachikulu, ndiponso kuli baja bamene bankala mumalo komanso mu mfinzi ya imfa, pali beve nyali onekela." 17 Kuchokela ntawi yamene ija Yesu anayamba kulalikila nakukamba kuti, "Tembenukani, chifukwa ufumu wa kumwamba wabwela pafupi." 18 Pamene Yesu anali ku enda mumbali ya mumana wa Galileya, ana ona babale babili, Simoni oitaniwa kuti Petulo, na Anduru, mubale wake, banali kuponya chogwililako nsomba mu nyanja, chifukwa banali banthu wogwila nsomba. 19 Yesu anakamba nabo kuti, "Bwelani, nikonkeni ine, ndipo nizakulengani kunkala bogwila babantu." 20 Pamene apo banasiya vogwililako nsomba naku konka Yesu. 21 Pamene Yesu anali kuyenda kuchoka kumalo uku anaona benangu babale babili, Yakobo mwana wa Zebediya, na Yohani mubale wake. Banali mu bwato na Zebediya tate wawo banali kukonza vogwililako nsomba vabo. Anabaitana, 22 pamene apo banasiya bwato na batate babo naku mukonka Yesu. 23 Yesu anayenda mu Galileya monse, kupunzisa mu ma Sinagogo yabo, kulalikila utenga wabwino wa ufumu, na kuchilisa matenda yosiyana siyana nakudwala pakati pa banthu. 24 Utenga wa eve unayenda konse ku malo ya Siliya, ndipo bantu banamuletela bantu bonse bamene banali na matenda nakubaba kosiyana-siyana, bonse baja bamene bana tengewa na vibanda, bonse ba makate nawonse bolemala. Yesu anabachilisa. 25 Magulu yakulu yanamukonka kuchokela ku malo ya Galileya, Dekapoli, Yelusalemu, na Yudeya, na konse kupitilila Yodani.