Mutu 15

1 Ndipo ninaona chizindikiro china m'mwamba, zazikulu ni zabwino: Panali angelo 7 ni mikwiyo 7, yamene ni zilango zothera, chifukwa mwa izi mkwiyo wa Mulungu uzatha. 2 Ninaona chamene chinaoneka monga nyanja ya galasi yosakaniza na muliro. Amene anaimilira pa mbali ya nyanja ni aja amene anapambana chilombo na fano lake, na nambala yamene iimilira zina lake. Anali na mitoliro yamene anapasidwa na Mulungu. 3 Anali kuimba nyimbo ya Mose, kapolo wa Mulungu, nyimbo ya mwana wa nkhosa: "Nchito zanu ni zabwino komanso za mphamvu, ambuye Mulungu, wa mphamvu zonse. Njira zanu ni zabwino ni za chilungamo, mfumu ya maiko onse. 4 Ndani wamene sazakuyopani, Ambuye, nakukweza zina lanu? Chifukwa inu nokha ndinu oyera. Maiko onse yazabwera kukupembezani cifukwa cha nchito zanu zoyera zomwe zavumbulusidwa." 5 Pambuyo pa izi zinthu ninaona, ndipo tenti ya mboni inaseguliwa ku mwamba. 6 Kuchoka pa malo oyera panachoka angelo 7 onyamula zilango 7. Anavala zobvala zoyera, zonyezimila ndi sashi ya golide yozungulira chifuwa chao. 7 Imozi mwa zamoyo zinai inapasa angelo 7 mbale za golide 7 za mkwiyo wa Mulungu, zamene zinkhala muyayaya. 8 Tempile inazaziwa na utsi wa ukulu wa Mulungu na mphamvu zake. Palibe amene analobamo mpaka pamene zilango zonse 7 zinatha.