Mutu 14

1 Ninaona na kuona mwana wa nkhosa oimilira pa phiri la Zion. Anali na anthu 144,000 amene anali na zina lake na zina la Atate ake yolembewa pa mphumi zao. 2 Ninamvera mau ochokera kumwamba omveka monga manzi yambiri na kugunda kwa mphamvu. Mau omwe ninamvera yanali monga anthu oliza mitoliro. 3 Anaimba nyimbo zasopano pamaso pa Mulungu, zamoyo zinai na akulu. Kunalibe wina opunzira nyimbo imeneyi koma chabe aja 144,000 omwe anaguliwa pa dziko la pansi. 4 Aba nibaja bamene sanazidese na akazi, cifukwa anazisunga ku chiwelewele. Niyaba amene alondola mwana wa nkhosa kulikonse kwamene ayenda. Awa anaguliwa kuchoka pa anthu ngati ana oyamba a Mulungu ni mwana wa nkhosa. 5 Palibe boza yamene inapezeka mkamwa mwao; niopanda chifukwa. 6 Ninaona mngelo wina akuuluka mu mwamba, amene anali na uthenga wa moyo ouza anthu onkhala pa ziko la pansi-ku maiko onse, mitundu yonse, chilankhulo na anthu. 7 Anaitana na mau a mphamvu, "yopani Mulungu na kumupasa ulemelero. Chifukwa nthawi ya chiweruzo chake chafika. Mulambileni, wamene anapanga kumwamba, dziko la pansi, nyanja, na nyenje za manzi." 8 Mngelo wina-mngelo wachiwiri- anasatira kukamba kuti, "Wagwa, wagwa Babylon wamphamvu, wamene anauza anthu onse kuti amwe vinyo wa zilakolako zake za chiwelewele." 9 Mngelo wina-mngelo wachitatu- anawalondola kukamba ati na mau okuwa, "ngati wina apembeza chilombo na chifano chake, na kupasiwa namba pa mphumi kapena pa zanja lake, 10 azamwa vinyo wa mkwiyo wa Mulungu, vinyo wamene waikiwa opanda kutirako manzi mu cup ya kukalipa kwake. Munthu amene azamwa azabvutika na muliro na sufule pamenso pa angelo na mwana wa nkhosa." 11 Utsi wa kunzunzika kwao upitilira ku mwamba nthawi zonse, ndipo sapumula usana na usiku-awa opembeza chilombo na fano lake, na aliyese amene analandira chizindikiro cha zina lake. 12 Apa pali kufunika kupilira kwa iwo amene ni oyera, amene akonkha malamulo ya Mulungu na chikhulupiliro mwa Yesu." 13 Ninamva mau kuchoka ku mwamba kukamba ati, "Lemba izi: Odala ni anthu amene anafa mwa ambuye." "Inde," ukamba mzimu,"kuti akapumule ku zolemesa zao, chifukwa nchito zao zizabalondola." 14 Ninayangana, ndipo panali makumbi yoyera. Ndipo onkhala pa makumbi anali ngati mwana wa munthu. Anali na kolona ya golide pa mutu pake na chikwakwa chonola ku manja yake. 15 Ndipo mngelo wina anatuluka mu nyumba ya Mulungu ndipo anaitana na mau okweza kuitana uja amene ali pa makumbi: "Tenga chikwakwa chako elo uyambe kujuba. Chifukwa nthawi yojuba yakwana, cifukwa zokolola pa ziko zapya." 16 Ndipo wamene anali pa makumbi anayamba kuyendesa chikwakwa pa ziko, ndipo ziko inakololedwa. 17 Mngelo wina anatuluka ku mwamba mu nyumba ya Mulungu; nayeve anali na chikwakwa. 18 Mngelo winanso anatuluka kuchoka pa guwa la zonunkhirisa, amene anali na ulamuliro pa muliro. Anaitana na mphamvu uja amene anali na chikwakwa chonola, "Tenga chikwakwa chako na kuika pamozi zidunswa za mpesa m'minda ya ziko, chifukwa mpesa wake wapya." 19 Mngelo anayendesa chikwakwa chake pa ziko nakutenga zidunswa za mpesa. Anaiponya motwera mpesa wa mkwiyo wa Mulungu. 20 Ndipo motwera mpesa munaponyewa panja pa mzinda, ndipo magazi anathiridwa kuchoka mwaicho kufika pakamwa pa akavalo, ma stadia 1,600.