Chapita 5

1 Mwamusanga pamene mafumu ya Amori kumbali ya kumazulo kwa Yolodani, na mafumu yonse ya Akanarli, bamene banali mumbali mwanya nja yaikulu, banamvela kuti Yehova anayumisa manzi ya mu Yolodani paka bana ba Israyeli anatauka, mitima yao yanasungunuka, ndiponso munalibe moyo anasalamo muli beve cifukwa ca bana ba Isreali. 2 Panthawi Yehova anakamba kuli Yoswa, ''panga manaifi ya miyala na kujuba bonse bana ba Israyeli kacibili.'' 3 Pamenepo Yoswa anapanga manaifi yamiyala nakujuba bonse bana ba Israyeli pa Gibeath, Haaraloth. 4 Ndiye cifukwa cake Yoswa anaba juba: Bonse bamuna bamene banacoka mu Eigipito, kufakilako nabazibambo bankhondo, anafa mucipululu munjila, pambuyo pacokokamu Eigipito. 5 Ingakuale bamuna bonse banacoka mu Eigipito banali bujubiwa, cimizi-mozi, palibe anyamata bana wila mucipululu munjila yocoka ku Eigpito anajubiwa. 6 Pakuti bana ba Israyeli banacoka zaka fote mu cipululu paka bathu bonse, niye, bonse bazibambo bankhondo banacoka mu Eigipito, anafa, cifukwa sanamvelela mav ya Yehova. Yehova analumbila kwaiwu kuti sazabasiya kuti babone malu yamene analumbila kuli makolo yao kuti azabapasa, ziko yoyendemo mkakana uchi. 7 Banali bana bao bamene Yehova anakulisa mumalo yao bamene Yoswa anajuba, cifukwa banali bakalibe kujubiwa munjira. 8 Pamene onse bana jubiwa, banasalila kwamene banali kugona paka bana pola. 9 Ndipo Yehova anakamba kuli Yoswa, ''Siku yalelo na cosapo manyazi ya Eigipito pali imwe, cifukwa chake, zina ya malo inaitaniwa Giligala kufika nalelo. 10 Bana ba Isreali banamanga misasa pa Giligala. Basunga paka pasiku ya fotini ya mwezi, mu mazulo, madimba ya yaliko. 11 Pasiku ya paska, siku yamene ija, bana dya vina vomela pa nthaka, mkate wopanda cotuposa na tiligu wokazinga. 12 Mana yanasiya pasiku banadya vomela pathaka. Kunaliba futi mana ya bana ba Israyeli, koma banadya vomelapanthaka ya kanani caka cija. 13 Pamene Yoswa anali pafupi na Yeliko, ananyamula mwenso yake na kuona, ndipo taona, mwamuna anaimilila pasogolo pake; anatenga panga nipo inali mumanja yake. Yoswa anayenda kuli yeva na ku kamba kuti,'' Uli naise kapene badani bathu? 14 Anakamba kuti,'' lyai. Popeza ndine bolamulila gulu ya nkhondo ya Yehova. Manje nabela.'' Pamenepo Yoswa anagwesa nkhope yake pansi kulambila nakukamba kuli yeve kuti, ''Akamba cani Ambuye wanga kuli mtumiki wake?'' 15 Bolamulila gulu ya nkhondo ya Yehova anakamba kuli Yoswa,'' vula nsapato zako ku mapazi yako cifukwa pamalo pamene waimilila ni poyela,'' ndiye zimene Yoswa anacita.