Chapita 24

1 Pamene Yeswa anasonkhaisa mitundu yonse ya Israyeli ku shechem nakuitana bakulu bonse ba Israyeli , basogoleli bao, boweluza, nabanchito, banazibwelesa pamene ya Mulungu. 2 Yoswa anakamba kuli banthu bonse,'' ndiye zamene Yehova akamba, Mulungu wa Israyeli, kukamba kuti makolo yanu kale benze kukhala kusidya ya mumana wa Euphrates - Terah, tate wa Abrahamu natate wa Nahor - na kulambila milungu zao. 3 Koma nunatenga batate bak kubacosa kusidya kwa Euphrates nakubasogolela muziku ya kanani na kumupasa bana bambili kupitila muli mwana wake Isaki. 4 Ndipo kwa Isaki ninapa Yakobo na Esau. Ninapasa Esau phili ya ziko yaku Seir kuitenga, koma Yakobo nabana bake banapita ku Eigipito. 5 Ninatuma Mose na Anroni, na kulanganga Eigipito namilila, zitapita izo, ninatulosani. 6 Ninatulusa makolo yanu mu Eigipito, ndipo unabwela kunyanja. Aigipito banapepeka beve nama galeta na bamuna bokwela bakavalo kufika ku nyanja yofiila. 7 Pamene makolo yanu babalila kuli Yehova, anaika mudima pakati kaiwe na mu Eigipito. Analengesa njanja, ibwele pali beve nakubavwinikila. munaona zamene ninacita mu Eigipito. Pamene munakhala mucipululu nthawi yaitali. 8 Ninakuletani kuziko ya Amoni, bamene banakhala kumbali ya Yolodani. Banamenyana naiwe, ninabapasa mumanja yako. Unalandila zio yao, ndipo ninababonga bonse pamenso panu. 9 Pamene Balaki umwana wa Zippor, mfumuya moabo, inanyumuka nakumenya Israyeli, Anatuma nakuitana Balamu mwana wa Beor, kutembelela iwe. 10 Koma sinamvelele kuli Balamu zoona, anakudalisa popeza ninaku pulumusa kukucosa manja mwake. 11 Anatauka pa Yolodani nakufika ku Yeliko. Basogoleli banamenyana naiwe, pamozi na Amori, Aperizi, Akanani, Iti, A Girgashita, A Hivitis, na A Tebusites. Ninakupasani kupambana pali beve nakubaika pansi paulamulilo wanu. 12 Ninatuma mavu pasogolo panu, yamene yanabacosa na mafumu yabili ya Amoni pamene yako, sizinacitike napanga yako kapene uta yako. 13 Ninakupasa malo yamene sunasebenzele na mizinda yamene sunamange, manje ukhalamo. Ukudya vipaso vamumunda na minda ya Olivi yamene sinashange! 14 Manje yopa Yehova nakulambila iye na ulemu onse na kukhulupilika: bononga milungu imene makolo banalambila kusidya ya Euphrate, na mu Eigipito, na Kulambila Yehova. 15 Ngati zibuneka zoipa mumenso yako kuti ulambila Yehova, zisankhile weka lelo wamene uzatumikila, kapena milungu ya makolo yanalambiliwa kusidya ya Euphrates, kapena milungu za Amori, mumalo mwabo mwamene ukhala. Koma kwaine na nyumba yanga, tizalambila Yehova. 16 Banthu banayankha nakukamba kuti,'' sitingaibale Yehova kutumikila milungu zina. 17 Popeza ni Yehova mulungu wathu anatikweza ku ticosa miziko ya Eigipito, kuticosa munyumba yaukapolo, amene anacita zizindikilo zikulu mumeneso mwathu, anatisunga munjila zonse zamene tinayenda, na pamaziko yonse tina pitamo. 18 Ndipo Yehova anacokapo pamenso pabanthu bonse, kufikilako ba Amori banakhala mu zio. Cifukwa cake naife tinalambila Yehova, popeza ni mulungu wathu. 19 Koma Yoswa anakamba kuli banthu kuti,'' simungatumikila Yehova, popeza nimulungu boyela; Ni mulungu wa nsanje,' sazakhulukilila zolakwa zanu na macimo yanu. 20 Ngati mwamusiya Yehova nakulambila milungo zina, pamene azatembunuka nakcita zoipa pali imwe. Azakusilizani, pambuyo pokucitilani zabwino. 21 Koma banthu banakamba kuli Yoswa,'' Iyai, tizalambila Yehova.'' 22 Pamenepo Yoswa anakamba kuli banthu,'' ndimwe mboni zaimwe weka kuti mwasankha Yehova, kumulambila iye,'' Banakamba,'' Ndife mboni.'' 23 Manje cosani milungu zacilendo zamene muli nazo, penyesani mitima yanu kuli Yehova, Mulungu wa Israyeli.'' 24 Banthu banakamba kuli Yoswa,'' tizalambila Yehova mulungu wathu tizamvela mau aya.'' 25 Yoswa anapanga cipangano nabantu siku ija. Anaika zinenelo na malamuno mu shechemu. 26 Yoswa analemba mau aya mubuku yacilamulo ca mulungu. Anatenga mwana ukulu na kuika pakati ka mtengo wa nthundu wamene unali pafupi malo yopa tulika ya Yehova. 27 Yoswa anati kuli banthu bonse,'' ona, uyu mwala uzkhala umboni wotisusa.Tamva mau yonse Yehova wakamba kuli ife. cifukwa cake izakhala mboni yokosusa, ngati uzafuma kukana mulungu wako. 28 Pamenepo Yoswa anabuza banthu kuti bayende, alibonse kucoloba cake. 29 Zitapita izi Yoswa mwana wa Nuni, mutumiki wa Yehova, anamwalila, nazaka 110. 30 Banamushika mumalile yacoloba cake, pa Timnath Serah, yamene ili muphili yaziko ya Eflemu, ku mpoto kwaphili ya Gaash. 31 Israyeli analambila Yehova masiku yonse ya Yoswa, na masiku yonse ya bakulu banakhala zaka kupamba na Yoswa, baja banabona vose vamene Yehova anacita kwa Israyeli. 32 Mafupa ya Yosefe, yamene ba ba Israyeli babaleta kucosa mu Eigipito - banaya shika pa shechem, mumalo yamunda mwamene Yakobo anagula kuti bana ba Hamor, tate wa shechem. Anaigula pa wanu handiledi ya siliva, ndipo ina khala coloba cabana ba Yosefe. 33 Eliyaza mwana wa Aaroni anamwalila nayeve. Banamushikila pa Gibeah, muzinda wa phinehasa mwana wake, yamene yenze inapasiwa kuli yeve. Inali muphili yaziko ya Eflemu.