mutu 4

1 2 3 1 koma ichi yona sana kondwele nacho ana kalipa maningi. 2ndipo yona ana pempela kuli YEHOVA na kukamba, ''ah,YEHOVA, sindiye ivi vamene nina kamba pamene nenze nikali ku ziko yanga? ndiye chifukwa chake nina yambilila na kuyesa ku taba kuyenda ku tashishi-chifukwa ninaziba kuti ndimwe MULUNGU wa mutima wabwino,wa chifundo,wosakalipa musanga ndiponso chikondi chanu ni chikulu, ndiponso mumazibweza ku kutuma chionongeko. 3mwa ichi manje, YEHOVA, nikupempani, nipokeni moyo wanga, pakuti chiliko bwino kuti nife kuchila kunkala wa moyo.'' 4 5 4 YEHOVA anakamba, ''nanga nichabwino kuti wakalipa maningi?'' 5ndipo yona ana choka mumu zinda nakunkala kumbali ya kumawa kwa muzinda. kwamene uko anazimangila tando nakunkala munyansi mwake muchimfwile kuti aone vamene viza chitika ku muzinda. 6 7 6YEHOVA anapanga msatsi na ku ukulisa pamwamba pa yona kuti chinkale chimfwile pa mutu pake kuchepesako mavuto yake. yona anamvela bwino chifukwa cha msatsi. 7koma MULUNGU anakonza nyongolosi kuseni seni. inaononga msatsi uja na msatsi una fota. 8 9 8 inafika ntau pamene zuba ina choka kuseni kokonkapo, MULUNGU anakonza mpepo yo kupya kuchoka kumawa. ndiponso, zuba inaseluka pa mutu pa yona ndiponso ana komoka. ndipo yona anafunisisa kuti amwalile. anazikambisa eka, ''nkasako kuti nife kuchila kunkala wa moyo.'' 9ndipo MULUNGU anakamba kuli yona, ''nanga nichabwino kuti wakalipa maningi pali msatsi?'' ndipo yona anakamba, 'nichabwino kuti na kalipa, kochita kufa nako,'' 10 11 10 YEHOVA anakamba, ''wachitila msatsi chifundo wamene suna shange, wamene suna sebenzele, kapena ku ukulisa. unakula musiku imozi ndiponso unafa musiku imozi. mwa ichi kwa ine, sininga nkale na chifundo pali ninive, muzinda uja ukulu, mwamene muli bantu kupitilila 120,000 bamene sibaziba ku siyana pali kwanja yabo ya kumazele na kwanja yabo ya manja, ndiposo na vinyama vambili?''