MUTU 26

1 Yobu anayanka na kuti, 2 "wamutandiza bwanji wamene alibe mpamvu! watandiza bwanji kwanja ilibe mpamvu! walimbikisa 3 bwanji wamene alibe nzelu na kumuuza mapunzilo yabwino! 4 na tandizo ya ndani yamene wakambila mau aba? ni muzimu wandani wamene wacoka muli iwe? 5 Bakufa bama njenjema, baja bali pansi pa manzi na zonse zonkala mukati. 6 Sheol ali cintaku pamenso pa Mulungu; cionongeko pa ceka ni cosabisika pa menso pake. 7 anapanga kumwamba pali malo yalibe kantu, na kufaka calo palibe ciliconse. 8 Amamanga manzi mu makumbi yake yotikama, koma makumbi siyamang'ambika pansi pake. 9 Amabisa pamwamba pa mwezi na kufakapo makumbi. 10 Anafaka malile yozungulila malo ya manzi monga mzela pakati pa kubala na mudima. 11 Vibumba va kumwamba vinjenjema na kudabwa pa kuzuzula kwake. 12 Amankazikisa bata pa msinje na mpamvu zake; pa kumvesesa kwake anavalilatu Rahabi. 13 Na mpamvu zake anapanga kumwamba kunkala kooneka bwino; kwanja kwake kunalasa njoka yotaba. 14 Yanganani, ivi ndiye koma kotela kwa njila zake; ni kung'ono bwanji kubelebesa kwamene timvelaza eve! ni ndani angamvesese kugunda kwa mpamvu zake?"