Mutu 14 1

1 Mfumu Davide anakota nakukala na zaka zambili, banamuvinikila nama blageti , koma eve sanamvele kufunda. 2 Ba nchito bake banakamba kuli eve, "Tisakilile bwana watu mfumu musikana mungono wamene saziba mwamuna. Amutumikile mfumu na kumusamalila eve. Agone mumanja mwake kuti bwana watu mfumu akale ofunda." 3 Ndipo beve bana sakila musikana okongola mukati mwa malile yonse ya Israeli. Beve banapeza Abishagi mu Shunammiti naku mupeleka kwa mfumu. 4 Musikana uyu anali okongola kwambili. Anatumikila mfumu nakumusamalila, koma mfumu sanamuzibe. 5 Pa ntawi ija, Adoniya mwana wa Hagiti anazikweza, anati, "Nizankala mfumu". Ndipo eve anakonzekela magaleta na apakavalo pamozi na amuna 50 kuti batamangile pasogolo pake. 6 Batate bake sibanamuvute, anati, "Ni Chifukwa chani wachita ivi kapena ivo?" Ndipo Adoniya anali muntu okongola maningi, obadwa pambuyo pa Absalomu. 7 Anakambilana na Joabu mwana wa Zeruya na wansembe Abiyatara. Ndipo bana mukonka Adoniya nakumutandiza eve. 8 Koma wansembe Zadoki, Benaya mwana wa Yehoyada, Nathani muneneli, Simeyi, Rei, na bamuna bampamvu ba Davide sanamukonke Adoniya. 9 Adoniya anapeleka nsembe ya nkosa, na ngombe, ngombe yamafuta pafupi na mwala wa Zoheleti, pafupi na Eni Rogeli. Anaitana abale bake bonse, bana bamuna ba mfumu, na bamuna bonse ba ku Yuda, banchito ba mfumu. 10 Koma sanayitane Nathani muneneli, Benaya, bamuna bampamvu, kapena Solomoni mubale wake. 11 Pameneapo Nathani anakamba na Bathsheba mai wa Solomoni, kukamba , Kodi simunamvele kuti Adoniya mwana wa Haggithi ankala mfumu, ndipo Davide bwana watu saziba? 12 Manje leka nikupase nzelu, kuti uzipulumuse weka na moyo wa mwana wako Solomoni. 13 Yendani kuli Mfumu Davide; mukambe naye, ' Bwana wanga mfumu, kodi simunalumbile kuli mutumiki wanu, na kuti, '' Zoona Solomoni mwana wako azankala mfumu pambuyo panga, naku nkala pa mupando wanga wachifumu? Nanga bwanji Adoniya akulamulila? '' 14 Pamene ukali kukamba na mfumu, ine nizabwela pambuyo pako ndipo nizasimikizila mau yako. ” 15 Ndipo Bathsheba anangena muchipinda cha mfumu. Mfumu anali okalamba kwambili, ndipo Abishagi mu Shunammiti ankatumikila mfumu. 16 Bathsheba anapepeza na kupasa ulemu ku mfumu. Pameneapo mfumu anakamba kuti, "Mufuna chani?" 17 Anakamba kuli eve, Bwana wanga, munalumbila kuli mutumiki wanu na Yehova Mulungu wanu, kuti, 'Zoona Solomoni mwana wako azankala mfumu pambuyo panga, azankala pa mupando wanga wachifumu. 18 Manje, onani, Adoniya ndiye mfumu, koma imwe bwana wanga mfumu simuziba. 19 Wapeleka nsembe za ngombe zambili, na ngombe zoyina, na nkhosa, ndipo ayitana bana bonse bamuna ba mfumu, wansembe Abiyatara, na Joabi mukulu wa ankhondo, koma sanayitane Solomoni mutumiki wanu. 20 Pali imwe, bwana mfumu yanga , Aisraeli bonse ayangana pali imwe, kuti mubauuze wamene azankhala pamupando wanu wachifumu, bwana wanga. 21 Chamene chizachitika , pamene bwana mfumu yanga akasamila zanja na makolo ake, ine na mwana wanga Solomoni tizankhala ngati bakawalala. ” 22 Pamene eve anali kukamba na mfumu , muneneli Nathani anabwela. 23 Ndipo anchito anauuza mfumu, "Muneneli Nathani afika." Pamene eve anabwela pamanso pa mfumu, anawelama pamanso pa mfumu na nkhope yake pansi. 24 Nathani anakamba kuti, ''Bwana wanga mfumu, kodi munakamba kuti, 'Adoniya azankhala mfumu pambuyo panga, nakuankhala pa mupando wanga wacifumu?' 25 Popeza lelo ayenda kupeleka nsembe ng'ombe zambili, zonenepa, na nkhosa. ndipo ayitana bana bamuna bonse ba mfumu, kazembe wa nkhondo, na Abyatara wansembe. Ba kudya na kumwa pasogolo pake, nakukamba kuti, 'Mfumu Adoniya ankhale na umoyo wautali !' 26 Koma ine , wanchito wanu, wansembe Zadoki, Benaya mwana wa Yehoyada, na Solomoni wanchito wanu, sanatiyitaneko ife. 27 Kodi bwana mfumu yanga mwachita izi kosatiuuza , banchito banu, kuti nidani wamene azankhala pa mupando wachifumu pambuyo pake?'' 28 Pameneapo Mfumu Davide anayankha nati, "Niyitanilenikoni Bathsheba kuti abwele kuli ine." Eve anabwela pamanso pa mfumu ndipo anayimilila pamanso pa mfumu. 29 Mfumu analumbila kuti, “Pali Yehova wamoyo, amene andiwombola ku mavuto yanga yonse, 30 monga ninalumbila kuli imwe na Yehova, Mulungu wa Israeli, kuti, 'Solomoni mwana wako azankhala mfumu pambuyo panga, ndipo azankhala pamupando wanga wachifumu mumalo mwanga, 'Nizachita izi lelo. " 31 Bathsheba anawelama mpaka nkhope yake pansi ndipo analemekeza mfumu nakukamba kuti, "Bwana wanga Mfumu Davide ankhale na umoyo osatha!" 32 Mfumu Davide anati, "Niyitanilenikoni Zadoki wansembe, Nathani mneneli, na Benaya mwana wa Yehoyada." Beve banabwela kuli mfumu. 33 Pameneapo mfumu nakamba kuti: “Tengani akapolo wa bwana wanu, ndipo mukwezeke mwana wanga Solomoni pa bulu yanga naku mupeleka ku Gihoni. 34 Lekani Zadoki wansembe na Nathani mneneli amuzoze ankhale mfumu ya Israeli nakuliza mapenga nakukamba kuti, Mfumu Solomoni ankhale na umoyo wautali! 35 Mwaichi muzabwela pambuyo pake, ndipo azabwela na nkunkhala pamupando wanga wachifumu. Namusankha kuti asogolele mfumu mumalo mwanga. Namusankha kuti ankhale musogoleli wa Israeli na Yuda. 36 ”Benaya mwana wa Yehoyada anayankha mfumu kuti, '' Chinkhale sochabe ! Lekani Yehova, Mulungu wa bwana mfumu yanga asimikizile izi. 37 Monga Yehova ankhala na bwana mfumu yanga, chinkhale sochabe kuli Solomoni, nakupanga mupando wake wachifumu koposa wa bwana wanga Mfumu Davide. ” 38 Pameneapo wansembe Zadoki, mneneli Nathani, Benaya mwana wa Yehoyada, na Kerethitesi na Pelethitesi banayenda naku kwezeka Solomoni pa bulu ya Mfumu Davide; banamutenga ku Gihoni. 39 Zadoki wansembe anatenga nyanga ya mafuta muchihema naku muzoza Solomoni. Pameneapo banaliza lipenga ndipo banthu bonse bana kamba kuti, “Mfumu Solomoni ankhale na umoyo wautali !” 40 Pameneapo banthu bonse banakwela patangu pake, ndipo banthu banaimba matolilo, na kukondwela na chisangalalo chachikulu; ndipo ziko inagwedezeka na phokoso zawo. 41 Adoniya na balendo bonse bamene banali naye banamvela pamene banasiliza kudya. Pamene Joabu anamvela kulila kwa lipenga anati, "Chifukwa nichani mu mzinda muli pokoso?" 42 Pamene anali kukamba , kunafika Jonathani mwana wa wansembe Abiyatara. Adoniya anati, genani, pakuti ndiwe munthu oyenela bwelesani uthenga wabwino.'' 43 Pameneapo Jonathani anayankha Adoniya kuti, “Bwana wathu Mfumu Davide wayika Solomoni kunkhala mfumu, 44 ndipo atumiza wansembe Zadoki, Nathani muneneli, Benaya mwana wa Yehoyada, ma Kerethitesi na Pelethitesi. Bana yenza Solomoni pa bulu yama mfumu Davide. 45 Zadoki wansembe na Nathani mneneli anamuzoza kuti ankhale mfumu ku Gihoni, ndipo abwela kwameneuko alikusangalala, pakuti mu muzinda wonse wasanduka phokoso. Ndiye phokoso yamene mwamvela. 46 Koma, Solomoni ankhala pamupando wachifumu. 47 Ndiponso, banchito ba mfumu anabwela kudalisa bwana wathu Mfumu Davide, nakukamba kuti, Mulungu wanu apange zina ya Solomoni yopambana kuchila zina yanu , nakupanga mupando wake wacifumu upose mupando wanu wacifumu. 48 Ndipo mfumu inagwada pansi pa bedi. Mfumu anakamba kuti, 'Alemekezeke Yehova, Mulungu wa Israyeli, wamene apasa lelo munthu wonkhala pamupando wanga wachifumu pasiku yalelo , na manso yanga yaona ichi.' 49 Pamenepo balendo bonse ba Adoniya anachita mantha. Banayimilila ndipo aliyense anapita njila yake. 50 Adoniya anayopa Solomoni, nakunyamuka, nakugwila nyanga za guwa ya nsembe. 51 Kenako anauza Solomoni kuti: “Adoniya ayopa Mfumu Solomoni, chifukwa wagwila nyanga za guwa yansembe, nati, 'Mfumu Solomoni anilumbilile kuti sazapaya mtumiki wake na lupanga.'' 52 Solomoni anakamba kuti, "Akazionesa ngati munthu oyenela, ngankhale sisi yake sizagwa pansi, koma ngati zoyipa zipezeka mwa eve, azafa." 53 Pameneapo mfumu Solomoni anatuma banthu, bamene anabwelesa Adoniya pa guwa ya nsembe. Anabwela nakugwadila Mfumu Solomoni, ndipo Solomoni anakamba kuti, "Yenda kunyumba kwako."